Chikondi Cha Sahabah wina pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)

Sahabah wina adabwera kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndikufuna kuti oh Mthenga wa Allah kodi Qiyamah idzafika liti? Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha pomufunsa kuti ndichani chomwe wachita sochinyeza kuikonzekera tsikulo?

Sahabah adayankha nati, Oh Mthenga wa Allah sindikudzitenga kuti ndiri ndi swalah Saum kapena sadaqah zochuluka zomwe ndapanga komanso ndimakonda Allah kwambiri komanso Mtumiki wake mu mtima mwanga, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kenako adati, ndithu pa tsiku lachiweruzo udzakhala limodzi ndi omwe umawakonda.

Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akulongosora, “Palibe chidawangondweretsa maswahabah radhiyallahu anhum kuposa mawu amenewa.”

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …