binary comment

Salaah Ya Amuna

Udindo wapamwamba womwe Swalah ili nawo m’moyo wa Msilamu siufunikira kufotokoza kulikonse. Mfundo yoti idzakhala gawo loyamba lomwe adzafunsidwe munthu pa tsiku la Qiyaamah ndi umboni wokwanira wotsimikizira kufunika kwake.

Sayyiduna Rasulullah (swallallahu alaih wasallam)

إن أول ما يحاسب الناس به يوم القيامة من أعمالهم الصلاة قال يقول ربنا جل وعز لملائكته وهو أعلم انظروا في صلاة عبدي أتمها أم نقصها فإن كانت تامة كتبت له تامة وإن كان انتقص منها شيئا قال انظروا هل لعبدي من تطوع فإن كان له تطوع قال أتموا لعبدي فريضته من تطوعه ثم تؤخذ الأعمال على ذاكم (سنن أبي داود، الرقم: 864)

Ndithu, chinthu choyambilira chimene Adzawerengedwe nacho anthu pa tsiku la Qiyaamah ndi Swalah yawo. Mbuye wathu adzanena kwa Malaaika (angelo) pomwe Mulungu Ngodziwa bwino pa chilichonse: “Yang’anani Swalah ya kapolo wanga; Ngati adaipemphera m’njira yokwanira ndi yangwiro kapena adaichita mopereŵera?” Ngati Swalah yake idaswalidwa mwangwiro ndi ndimokwanilira, malipiro ake onse adzalembedwa kwa iye. Adzanena kwa Malaa ́ikah (angelo): “Mubwezereni kupereŵeka mu Swalaah yake ya fardh kudzera mu Swalaah yake ya nafl. Pambuyo pake, ibaadaah zina zidzatsata ndondomeko yomweyi.”


[1] هذا الحديث سكت عنه أبو داود والمنذري (مختصر سنن أبي داود، 1/306)

Check Also

Rakaah Yachiwiri

1. Mukamanyamuka pa sajdah, choyamba nyamulani chipumi ndi mphuno, kenako zikhato ndikumalizira mawondo. 2. Pamene …