1. Pambuyo pa sajda yachiwiri ya rakaah yachiwiri, khalani tawarruk kutanthauza kukhala ndi thako lakumanzere ndikutulutsa phazi lakumanzere pansi pa mwendo wakumanja. Phazi lakumanja likhale lowongoka ndi zala ziyang’ane kuchibla.
Chidziwitso : Kukhala m’malo a tawarruk kumagwiranso ntchito pa swala yomwe ili ndi qa’dah imodzi mwachitsanzo rakaah ziwiri ndi qa’dah yomaliza ya rakaah zinayi. Koma Qaadah yoyamba ya rakaah zitatu kapena zinayi, wina adzakhala mwa iftiraash, kutanthauza kuti phazi lakumanja lidzawongoka zala zitalunjika ku Qibla ndipo wina adzakhalia phanzi lamanzere.
2. Pokhala tashahhud, tsekani zala zitatu zakumanja mwachitsanzo chala chapakati ndi zala ziwiri zomwe zili pambali pake. Chala cha shahaadah (chala cholozera/chankomba phala) ndi chala chachikulu zidzasiyidwa zotambasura koma chala chachikulu chidzalumikizidwa m’mbali mwa chala cha shahaadah. Ponena za dzanja lamanzere, siyani zala zotambasura Ndikulisiiya dzanja lanu m’mphepete mwa ntchafu. Zala zidzasiyidwa m’mene zimakhalira ndipo sizidzalumikizana pamodzi.
3. Iwerengeninso tashahhud:
َلتَّحِيَّاتُ الْمُبَارَكَاتُ الصَّلَوَاتُ الطَّيِّبَاتُ لِلّٰهِ السَّلَامُ عَلَيْكَ أَيُّهَا النَّبِيُّ وَرَحْمَةُ اللّٰهِ وَبَرَكَاتُهُ سَلَامٌ عَلَيْنَا وَعَلٰى عِبَادِ اللّٰهِ الصَّالِحِيْن أَشْهَدُ أَنْ لَا إِلٰهَ إِلَّا اللهُ وَأَشْهَدُ أَنَّ مُحَمَّدًا رَّسُولُ اللّٰهِ
Malonje odalitsika, Swalah yabwino zipite kwa Mulungu, Mtendere ukhale pa iwe Mneneri, ndi chifundo cha Mulungu ndi chilungamo Chake, mtendere ukhale pa ife, ndipo Mulungu Ngopambana, ndipo Mulungu Ngopambana.
4. Pamene mukunena mawu oti Illallah tukulani chala chanu chankomba phala ndipo musachigwetse mpaka kumapeto kwa Qa’da. Pa nthawi yokweza chala, yang’anani chala chanu mpaka kumapeto kwa Swalaah.