لِإِيلفِ قُرَيْشٍ ﴿١﴾ اِلٰفِهِمْ رِحْلَةَ الشِّتَآءِ وَالصَّيْفِ ﴿٢﴾ فَلْيَعْبُدُوا۟ رَبَّ هٰذَا الْبَيْتِ ﴿٣﴾ الَّذِىٓ أَطْعَمَهُم مِّن جُوْعٍ وَاٰمَنَهُمْ مِّنْ خَوْفِۭ ﴿٤﴾
Chifukwa cha chitetezo cha ma Quraishi, chitetezo chimene amasangalala nacho m’maulendo awo m’miyezi yachisanu ndi m’nyengo yachilimwe. Kotero akuyenera kupembedza Mbuye wa nyumba yopatulika (Ka’aba), yemwe adawapatsa chakudya chothetsa njala yawo ndi chitetezo ku mantha.
M’nthawi ya Chisilamu chisanayambe, kuba, kuphana komanso kumenyana pakati pa anthu zinali zofala komanso zinali zofala pakati pa mafuko a m’dziko la Arabia. Choncho, poyenda kuchokera kumalo ena kupita kwina, anthu ankaopa kuukiridwa ndi adani awo kapena kutsekeredwa m’njira ndi achifwamba.
Komabe, malingana ndi fuko la ma Quraishi, adali kulemekezedwa kwambiri kuchokera ku mabanja ndi mafuko onse okhala mu Arabiya chifukwa cha udindo wawo wapamwamba wokhala oyang’anira Kaabah Shareef. Anthu ankalemekeza kwambiri Ka’bah Shareef ndi oyang’anira Ka’bah Shareef. Choncho, anthu sankasokoneza magulu a ma Quraishi ochita malonda ndipo ankawalora kuyenda momasuka komanso motetezeka pomwe magulu ena apaulendo anali kulandidwa, kubedwa ndi kuphedwa. Choncho, apaulendo awo ankayenda momasuka ku Yemen m’nyengo yachisanu, ndi ku Syria m’nyengo yachilimwe, popanda mantha, akubwerera ndi mitundu yonse ya zokolola, chakudya ndi zofunika zina zimene anthu a ku Makka Mukarramah ankazifuna.
Kunena zoona, Ka’bah Shareef ndiyomwe idabweretsa chitetezo cha ma Quraish ndi kupambana kwawo pazachuma.
لِإِيلفِ قُرَيْشٍ ﴿١﴾ اِلٰفِهِمْ رِحْلَةَ الشِّتَآءِ وَالصَّيْفِ ﴿٢﴾
Chifukwa cha chitetezo cha ma Quraishi, chitetezo chimene ankasangalala nacho m’maulendo awo m’miyezi yachisanu ndi m’nyengo yachilimwe.
M’surayi Allah Taala akukumbutsa ma Quraishi zabwino ziwiri zapadera za Allah Ta’ala zomwe zili pa iwo; kuchuluka kwa chitetezo ndi kulemera kwabwino. Atawafotokozera zabwino ziwirizi, Allah Taala akuwauza kuti amumvere Iye ndipo asapembedze wina aliyense kusiya Iye.
Kuchokera apa, tikuphunziranso kuti ma Quraish adadalitsidwa ndi ulemu ndi ulemelero wowonjezera ndi Allah Ta’ala poyerekeza ndi ena. M’ Hadith zidanenedwa kuti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa sallam) adati:
“Kuchokera kwa ana a Hazrat Ismaa’eel (’alaihis salaam), Allah Ta’ala adawasankha Banu Kinaanah, ndipo mwa Banu Kinaanah Allah Ta’ala adawasankha ma Quraish, ndipo mwa ma Quraishi, Allah Ta’ala adasankha Banu Haashim, ndipo mwa Banu Haashim, Allah Ta’ala adandisankha.”
Choncho ma Quraishi adapatsidwa ulemu ndi ulemelero waukulu ndi Allah Taala Mwiniwake. Nthawi zambiri, ulemu ndi mdalitso umenewu umapezeka kudzera mu chigamulo cha Allah Ta’ala. Palibe amene angafunse funso loti: “N’chifukwa chiyani ma Quraishi adapatsidwa udindo wapamwamba kuposa ena?” Ndipo ichi ndi chisomo cha Allah Taala, ndipo amapereka chisomo chake kwa amene wamfuna.
Komabe, chifukwa chodziwikiratu chomwe ma Quraish adapatsidwira udindo wapamwambawu powayerekeza ndi ena n’chakuti, iwo adali ndi makhalidwe ambiri akulu ndi apamwamba monga kukhulupirika, kuyamika ndi kuthokoza, kusamalira anthu ndi kuthandiza ofooka ndi oponderezedwa. Makharidwe abwino amenewa komanso osililikawa adali odziwika bwino mwa ma Quraish. Kotero Allah adawasankha iwowa kukhala oyang’anira nyumba yake.
فَلْيَعْبُدُوا۟ رَبَّ هٰذَا الْبَيْتِ ﴿٣﴾ الَّذِىٓ أَطْعَمَهُم مِّن جُوْعٍ وَاٰمَنَهُمْ مِّنْ خَوْفِۭ ﴿٤﴾
Kotero amupembedze Mbuye wa nyumba yopatulika (Ka’aba), yemwe adawapatsa chakudya chothetsa njala yawo ndi chitetezo ku mantha.
M’surayi Allah Ta’ala akuuwonetsa Ummah wa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa sallam) njira yopezera chisomo Chake chapadera.
Njira yopezera chisomo chapadera cha Allah Taala ndiko kusonyeza kumvera Allah Taala ndi kumthokoza. Munthu akakhala womvera Allah Taala ndi kuthokoza, Allah Taala amamudalitsa ndi zabwino ziwiri zazikulu.
Ubwino woyamba ndikuti Allah Taala amamudalitsa ndi riziki la Halaal ndikumuteteza ku njala ndi chilala. Momwemonso Allah Taala amampatsa iye mochuluka mu chuma chake ndi riziki lake.
Chisomo chachiwiri ndichakuti Allah Taala amampatsa chitetezo m’moyo wake ndi chuma chake.
M’ndime ina ya Qur’aan Majeed, Allah Ta’ala watchula fanizo lomwe gulu lidali lodalitsidwa ndi zabwino zonse zochokera kumbali kwa Allah Ta’ala.
وَضَرَبَ اللَّهُ مَثَلًا قَرْيَةً كَانَتْ آمِنَةً مُّطْمَئِنَّةً يَأْتِيهَا رِزْقُهَا رَغَدًا مِّن كُلِّ مَكَانٍ
Ndipo Mulungu akupereka fanizo: Mzinda omwe udali wamtendere, riziki lake likuudzera mochuluka kuchokera paliponse.
Koma (anthu a mumzindawo) adatsutsa zabwino za Mulungu. Choncho Mulungu adaulawitsa njala ndi mantha (amene adauphimba) ngati Chovala, kukhala malipiro a Zomwe adali kuchita.
فَكَفَرَتْ بِأَنْعُمِ اللَّهِ فَأَذَاقَهَا اللَّهُ لِبَاسَ الْجُوعِ وَالْخَوْفِ بِمَا كَانُوا يَصْنَعُونَ
“Njala ndi mantha zowaphimba ngati chovala” zomwe zatchulidwa m’ndime imeneyi zimatanthauza kuti njala ndi mantha zinali zamphamvu kwambiri moti zinali ngati zawaveka ndi kuwaphimba kuyambira kumutu mpaka kumapazi.
Choncho, tikuphunziranso kuti njira yopezera zabwino za Allah Taala ndi kusunga mtendere wa Allah Ta’ala kukhala wokhazikika ndi kuuteteza kuti zisagwidwe, ndikukhala omvera Allah Ta’ala ndi kusonyeza chiyamiko ndi kukhulupirika kwa Allah Taala chifukwa cha ubwino wake nthawi zonse.
Imaam Jazaree (rahimahullah), Imaam wodziwika bwino wa qiraat, akunena kuti pa nthawi yamantha, zimalimbikitsidwa kuwerenga Surah Quraish.
Mu Tafseer Mazhari, Qaari Thanaaullah (rahimahullah) akuti, “Shaykh wanga, Hazrat Mirza Mazhar Saheb (rahimahullah), adandilangiza kuti pa nthawi yomwe munthu wagwidwa ndi mantha, awerenge surayi.” Qaari Thanaaullah (rahimahullah) akunenanso kuti, “Ndidachita izi ndipo ndidaziwona kuti ndizothandiza kwambiri komanso zopindulitsa.”