Kuwerenga Duruud ngati waiwala China chake

عن أنس رضي الله عنه قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: إذا نسيتم شيئا فصلوا علي تذكروه إن شاء الله تعالى (أخرجه أبو موسى المديني بسند ضعيف كما في القول البديع صـ 448)

Sayyiduna Anas (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adati: ngati waiwala chinachake udziwerenga duruud kundifunira zabwino, ngati Allah angafune udzakumbukira.

Moyo Ndi Chuma Cha Sayyiduna Abu Bakr (Radhiyallahu Anhu) ziperekedwa Nsembe Chifukwa Cha Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasallam)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti tsiku lina lake Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “palibe chuma cha munthu chomwe chidandithandiza kwambiri kuposera chuma cha Abu Bakr Siddeeq (radhiyallahu anhu).” Pakunva zimenezi Sayyiduna Abu Bakr (radhiyallahu anhu) adayamba kulira kwambiri ndipo adati, “oh Mtumiki wa Allah (sallallahu alaih wasallam), chuma changa ndi moyo wanga zonse ndi zanu.” (Sunan Ibnu Majah, #94)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …