Nyumba ya Bibi Faatimah (radhiyallahu anha) idali potalikirako ndi nyumba ya Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Tsiku lina Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamuuza kuti “khumbo langa ndiloti udzikhala nane pafupi” Bibi Faatimah (radhiyallahu anha) adayankha nati, Nyumba ya Haarithah ili pafupi ndi yanu, ngati mungamupemphe kuti tisinthanitse ndi yanga adzavomera mwansangala. Tidasinthanapo kale m’mbuyomu ndiye ndikuchita manyazi kuti ndimupemphenso”.
Ngakhale zidali choncho olemekezeka Haarithah (radhwiyallahu anhu) adazadziwabe kuti Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) amafuna Faatimah atamakhala naye pafupi. Ulendo wina anabwera kwa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) ndikumuuza kuti: Oh Mthenga wa Allah, ndamvetsedwa kuti mukukhumba mutamakhala moyandikana ndi Faatimah, nyumba zanga ndi zimenezi, palibe nyumba ina yomwe ili pafupi ndi inu kupatula nyumba zangazi, titha kusinthana ndi Faatimah nyumba iliyonse m’nyumbazi, Oh Mthenga wa Allah, chomwe mungapemphe ndikutenga kuchokera kwa ine ndichomwe chingakhale chokondeka kwa ine kuposa chomwe mungandisiile,”
Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adamvomera ndikumuuza kuti,” ndikudziwa kuti zomwe ukuyankhula zikuchokera pansi pa mtima”. Ndipo Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adamangira Dua.