Kapempheredwe ka Azimayi

Qadah ndi Salaam

7. Ngati ili qa’dah yomaliza, werengani tashahhud, Salawaat Ebrahimiyyah (Durood Ebrahim) ndipo kenako pangani duwa. Duruud Ebrahimiyyah (Durood Ebrahim) ili motere: اَللّٰهُمَّ صَلِّ عَلٰى مُحَمَّدٍ وَّعَلٰى اٰلِ مُحَمَّدٍ كَمَا صَلَّيْتَ عَلٰى إِبْرَاهِيْمَ وَعَلٰى اٰلِ إِبْرَاهِيْمَ وَبَارِكْ عَلٰى مُحَمَّدٍ وَّعَلٰى اٰلِ مُحَمَّدٍ كَمَا بَارَكْتَ عَلٰى إِبْرَاهِيْمَ وَعَلٰى اٰلِ إِبْرَاهِيْمَ فِيْ الْعَالَمِيْنَ …

Read More »

Rakaah Yachiwiri

1.Pamene mukudzuka kuchoka pa sajdah, choyamba kwezani chipumi ndi mphuno, kenako zikhato kenako mawondo. 2.Pamene mukuimirira Rakaah yachiwiri, gwirani pansi poika manja anu onse pansipo kuti muthandizikire kunyamuka. 3.Pempherani rakaah yachiwiri monga mwa nthawi zonse (kupatula Dua-ul Istiftaah). Qadah ndi Salaam 1. Pambuyo pa sajda yachiwiri ya rakaah yachiwiri, khalani …

Read More »

Jalsah

1. Nenani takbira ndipo khalani tsonga (jalsah). 2. Phazi lakumanja muliyimike ndi zala zake ndikuyang’anitsa ku qibla. phazi lakumanzere muligoneke ndikulikhalira. 3. Khalani mokumanitsa ntchafu zanu pamodzi (muzikumanitse). 4. Ikani manja anu pa ntchafu ndi zala pamodzi ndipo nsonga za zala zanu zikhale m’mphepete mwa mawondo. 5. Yang’anani malo omwe …

Read More »

Sajdah

1. Nenani takbira ndikupita pa sajdah. 2. Gwirani manja anu m’mawondo pamene mukupita pa sajdah 3. Choyamba ikani mawondo pansi, kenako zikhatho, ndipo pomalizira pake chipumi ndi mphuno pamodzi. 4. Siyani zala zotsekeka moyang’anitsa ku chibla. 5. Ikani zikhatho zanu pansi m’njira yoti zala zifanane ndi makutu ndipo mbali zigwirizane …

Read More »

Ruku ndi I’tidaal

6. Timisomali tamapazi onse awiri akhale pamodzi. Ngati izi ndizovuta, ndiye kuti ziyenera kusungidwa moyandikana momwe zingathekere(momwe mungakwanitsire). 7. Yang’anani malo a sajdah m’maimidwe a ruku (pamene muli pa ruku). 8. Werengani tasbeeh katatu kapena nambala ina iliyonse yosagawika pawiri.   سُبْحَانَ رَبِّيَ الْعَظِيْم Subhaana rabbiyal A’dhwiim Kuyeretsedwa konse ndi …

Read More »

Ruku ndi I’tidaal

1. Mukamaliza kuwerenga Surah Faatihah ndi surah ina, yimani kaye pang’ono ndipo pambuyo pake kwezani manja (monga momwe tafotokozera mu takbeeratul ihraam) uku mukunena takbira ndikupita pa rukuu. Zindikirani: Takbeeraat intiqaaliyyah (takbeer yomwe imanenedwa posuntha kuchoka ku kaimidwe kena kupita ku kena) iyenera kuyambika munthu akangoyamba kusuntha kupita ku kaimidwe …

Read More »

Qiyaam

10. Mukangoyamba Swalaah, werengani Dua-ul Istiftaah chamuntima: وَجَّهْتُ وَجْهِيَ لِلَّذِيْ فَطَرَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ حَنِيْفًا مُسْلِمًا وَمَا أَنَا مِنَ الْمُشْرِكِيْنَ إِنَّ صَلَاتِيْ وَنُسُكِيْ وَمَحْيَايَ وَمَمَاتِيْ لله ِرَبِّ الْعَالِمِيْنَ لَا شَرِيْكَ لَهُ وَبِذلِكَ أُمِرْتُ وَأَنَا مِنَ الْمُسْلِمِيْنَ Ndatembenukira nkhope yanga kwa Yemwe adalenga thambo ndi nthaka, ndikukhalabe panjira yoongoka popanda kusokonekera, ndikugonjera …

Read More »

Qiyaam

1. Yang’anani kuchibula. 2. Sungani mapazi pamodzi kapena pafupi momwe mungakwanitsire. Onetsetsani kuti mapazi ayang’ana kuchibla. 3. Pambuyo pake, pangani Niya ya Swalah yomwe mukuswali ndipo kwezani manja anu mpaka zala zanu zazikulu zigwirizane ndi nsonga zamakutu ndipo nsonga za zala zanu zikhale molingana ndi kumtunda kwa makutu anu. 4. …

Read More »

Swalaah Isanayambe

1. Chisamaliro chapadera chiyenera kutengedwa povala moyenera pa Swalaah. Mkazi ayenera kuvala chovala choterocho chomwe chidzabisa thupi lake lonse ndi tsitsi lake. Ndikusadzipatsa ulemu iye mwini kuvala zovala zothina zomwe zimasonyeza mmene thupi lake lilili kapena kuvala zovala zopyapyala zimene zingachititse kuti ziwalo zenizeni ziwonekere. Ngati chovalacho chili chooneka kuti …

Read More »

Mfundo Ya Imaam Shaafi’ee

Imaam Shaafi’e (rahimahullah) walemba mu chitabu chotchedwa Ikhtilaaful Hadith kuti: Sitikudziwa mwa akazi olemekezeka a Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) kusiya nyumba zawo ndikupita kunzikiti kukaswali Swalaah ya Jumuah kapena Swalah ina iliyonse, ngakhale kuti adali akazi olemekezeka a Sayyiduna Rasulullah chifukwa cha udindo wawo wapadera ndi ubale wawo ndi Mtumiki …

Read More »