Sajdah

1. Nenani takbira ndikupita pa sajdah.

2. Gwirani manja anu m’mawondo pamene mukupita pa sajdah

3. Choyamba ikani mawondo pansi, kenako zikhatho, ndipo pomalizira pake chipumi ndi mphuno pamodzi.

4. Siyani zala zotsekeka moyang’anitsa ku chibla.

5. Ikani zikhatho zanu pansi m’njira yoti zala zifanane ndi makutu ndipo mbali zigwirizane ndi mapewa.

6. Ziikeni ziwalo za thupi lanu moyandikana ndikuzikanikiza mwamphamvu osalola kusiyana kulikonse pakati.

7. Kumanizani mimba yanu ndi ntchafu zonse ndi ndikuika mikono yanu m’mbali.

8. Miyendo yonse iwiri ikhale pansi ndi zala zitayang’ana ku Qibla. Sungani mpata wa dzanja limodzi pakati pa mapazi anu pamene muli pa sajdah.

9. Yang’anani maso pa malo opangira sajdah.

10. Werengani tasbeeh katatu katatu kapena nambala ina iliyonse yosagawika pawiri:

سُبْحَانَ رَبِّيَ الْأَعْلٰى

Subhaana Rabbiyal A’laa

kuyeretsedwa konse ndi kwa Mbuye wanga, Wapamwambamwamba.

Check Also

Ruku ndi I’tidaal

6. Timisomali tamapazi onse awiri akhale pamodzi. Ngati izi ndizovuta, ndiye kuti ziyenera kusungidwa moyandikana …