Dua

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 4

9. Pamene mukupanga dua, mtima wanu uyenera kukhala olunjika ndi kukhala ndi chidwi kwa Allah, Mtima wanu usakhale osalabadira komanso osaganizira pamene mukupanga dua. Musamamwaze maso kuwayang’ana anthu pamene mukupanga dua. Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Pemphani kwa Allah motsimikiza ndi mwachiyembekezo kuti …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 3

6. Popanga dua, musagwiritse ntchito njira yokayikira. Mwachitsanzo, musanene kuti: “E Allah, ngati Mukufuna kundikwaniritsira zosowa zanga kwaniritsani; Olemekezeka Abu Hurayrah (Radhwiyallahu anhu) adasimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam adati; popanga dua m’modzi wa inu asanene kuti Ndichitireni chifundo ngati Mukufuna, ndikhululukireni ngati Mukufuna ndi ndipatseni mariziki ngati mujufuna.’ m’malo …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2

2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu). Olemekezeka Salmaan Faarsi (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: Ndithu Allah ndi olemekezeka, okoma mtima kwambiri komanso owolowa manja. Ulemu Wake ndiwakuti amaona kuti ndi zotsutsana ndi ukulu Wake ndi chifundo Chake …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 1

1. Yambani dua pomulemekeza Allah kenako mudzamuwerengera duruud Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam). Pambuyo pake, modzichepetsa ndi ulemu onse, mudzapempha zosowa zanu pamaso pa Allah. Olemekezeka Fadhaalah bin Ubaid (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti nthawi ina Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adakhala munzikiti pamene munthu wina adalowa ndikuyamba kuswali. Kenako adapempha nati: “Oh, …

Read More »

Nthawi Zomwe Ma Dua Amayankhidwa

Nthawi ya Azaan ndi Pamene Magulu Awiri Akumana Pankhondo Olemekezeka Sahl bin Sa’d (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallah alaihi wasallam) adati: “Pali nthawi ziwiri zomwe madua sangakanidwe kapena nthawi zambiri sangapande osayankhidwa; pa nthawi ya Azaan ndi pamene magulu awiri ankhondo akumana pankhondo.”[1] Pakati pa Azaan ndi Iqaamah Olemekezeka …

Read More »

Anthu Omwe Ma Duwa Awo Amayankhidwa 2

Munthu Yemwe Akudwala Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu anahu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Mukakumana ndi odwala, mupempheni kuti akupangireni duwa chifukwa dua yake ili ngati dua ya angero (chifukwa cha kudwalako, machimo ake amakhululukidwa), choncho akufanana ndi angelo pokhala opanda machimo, ndipo potero pempho lake lidzalandiridwa mwachangu). Yemwe Amapanga …

Read More »

Anthu Omwe Ma Duwa Awo Amayankhidwa 1

Makolo, Wapaulendo ndi Oponderezedwa Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Ma dua atatu ndi otero kuti pangavute bwanji adzalandiridwa; dua ya bambo (kapena mayi, pa mwana wawo), dua ya musaafir (munthu wapaulendo) komanso dua ya oponderezedwa.”[1] Munthu Osala kudya komanso Mtsogoleri Wachilungamo Olemekezeka Abu …

Read More »

Kufunika Kwa Dua 3

Njira Yopezera madalitso Ndi kudzitetezera Kwa Adani Olemekezeka Jaabir bin Abdillah akusimba kuti Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adauza maSwahaabah kuti: “Kodi sindingakusonyezeni njira yoti mupulumutsidwe kwa adani anu ndi kulandira zochuluka m’zimene muli nazo? Tembenukirani kwa Allah usiku ndi usana chifukwa dua ndi chida cha okhulupirira.”[1] Mngelo Apangira Dua Munthu …

Read More »

Kufunika Kwa Dua 2

Dua Kupindulira Munthu Mnthawi ino ndi Mtsogolo Olemekezeka Ibnu Umar (Radhwiyallahu anhuma) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Dua imapindulitsa pakalipano komanso mtsogolo. Choncho, inu akapolo a Allah, pirirani popempha.[1] Yemwe amapanga Dua nthawi zonse Amapindula Olemekezeka Abu Sa’iid Khudri (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: …

Read More »

Kufunika Kwa Dua 1

Chida cha okhulupirira Olemekezeka Ali (Radhwiyallahu anhu) anasimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati:“Dua ndi chida cha okhulupirira, Mzati wa Dini, ndi Nuur (kuwala) yakumwamba ndi pansi.”[1] Dua ndi gwero la Ibaadah Olemekezeka Anas (radhwiyallahui anhu) akusimba kuti Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adati:”Dua ndiye maziko a ibaadah.”[2] Allah amasangalatsidwa pamene …

Read More »