Zizindikiro Khumi Zikuluzikulu Za Qiyaamah
Monga zilili kuti pali zisonyezo zambiri zing’onozing’ono za Qiyaamah zomwe zalembedwa Mmahaadith, momwemonso pali zisonyezo zikuluzikulu zambiri zomwe zatchulidwanso Mmahaadith. Zizindikiro zikuluzikulu ndi zinthu zofunikira kwambiri zomwe zidzachitike pa dziko lapansi pano Qiyaamah isanafike ndipo zidzalengeza kuyandikira kwa Qiyaamah. Ma Muhadditheen aika kubwera kwa Imam Mahdi (radhiyallahu ‘anhu) ngati chizindikiro choyamba chachikulu cha Qiyaamah. (Ishaa’ah tsamba 191)
Zina mwa zisonyezo zikuluzikulu za Qiyaamah, muli zisonyezo zazikulu khumi zomwe Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adanenetsa mu Hadith yotsatirayi. Ngati munthu akuyenera kusinkhasinkha pa zizindikiro zazikulu khumi izi, adzazindikira kuti ndi zoopsya kotero kuti zotsatira zake zidzazungulira dziko lonse lapansi kapena gawo lalikulu la dziko lapansi.
Olemekezeka Huzaifah bun Usaid (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adati: “Nthawi ina Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adadza kwa ife, maSwahaabah (Radhiyallahu ‘anhum), pamene tinkakambirana. Olemekezeka Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adatifunsa kuti: “Mukukambirana chiyani?” Ife tidati: “Tikukambirana za nkhani ya Qiyaamah.” Atamva izi, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Ndithu, Qiyaamah siidzachitika mpaka utaona zisonyezo zikuluzikulu khumi.
“Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adatchura zizindikiro khumi zikuluzikulu monga: Utsi (umenewu udzakhala mtundu wa nkhungu kapena utsi umene udzadzadze padziko lonse kuchokera kumwamba omwe udzachititse Asilamu kugwidwa ndi chimfine ndipo makafiri adzakomoka), kutuluka kwa Dajjaal, kutuluka kwa chilombo, kutuluka kwa dzuwa kuchokera kumadzulo, kutsika kwa Nabiy Isa (‘alaihis salaam), Kudza kwa Ya’juj ndi Ma’juuj, kumira katatu kwa nthaka; Kumira kum’mawa, kumira kumadzulo ndi kumira ku Arabian Peninsula. Chizindikiro chomaliza ndi moto omwe udzabuke ku Yemen ndikuwathamangitsira anthu kuchigwa cha Mahshar (Syria). (Sahiih Muslim #2901)
Mwa zisonyezo zikuluzikulu khumi zatchulidwa mu Hadith iyi, choyambilira kubwera ndi kutulukira kwa Dajjaal.
Kutulukira kwa Dajjaal
Zanenedwa mu Hadith kuti kuyambira ku chiyambi cha nthawi mpaka kufika pa Qiyaamah, mayesero a Dajjaal adzakhala m’gulu la mayesero aakulu kwambiri amene dziko lidzakumane nawo. Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati: “Kuyambira pamene adalengedwa Nabiy Aadam (‘alaihis salaam) mpaka tsiku la Qiyaamah, palibe mayesero amene adzakhale aakulu kuposa mayesero a Dajjaal.” (Mu’jam Kabîr #451)
Popeza Dajjaal adzatulukira mu Ummah uwu – Ummah wa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) – adzayenera kulimbana ndi fitnah yaikuluyi. Kuopsya kwa fitnah ya Dajjaal padziko lonse lapansi tingakumvetse pozindikira kuti Nabii aliyense adadziwitsa ummah wake za kutulukira kwa Dajjaal ndi kuonongeka kwakukulu komwe adzadzetse pa dziko lapansi.
Olemekezeka Abdullah bin Umar (Radhiya Allaahu ‘anhuma) adanena kuti nthawi ina Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati: “Ndithu ine ndikukuchenjezani za Dajjaal, ndipo palibe Nabii wina kupatula kuti adachenjeza anthu ake za Dajjaal, ngakhale Nabi Nuuh (‘alaihis salaam) adawachenjeza anthu ake za Dajjaal. Komabe, ndikuuzani zina zoonjezera zokhudza Dajjaal zomwe palibe Nabii amene adauza anthu ake – dziwani kuti Dajjaal ali ndi chilema m’diso limodzi, ndipo Allah Ta’ala si amene ali ndi chilema m’diso limodzi (Iye ndi opanda chilema chilichonse).” (Sunan Tirmizi #2235)
Kodi Dajjaal ndi ndani?
Anthu ena amavomereza kuti Dajjaal ndi dongosolo lapadziko lapansi pomwe ena amaona kuti ndi Jinn. Pali gulu lachitatu lomwe likuona kuti Dajjaal ndi osakanikirana (munthu ndi ziwanda). Komabe, chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah ndikuti Dajjaal ndi munthu wina wake amene adzatuluke mu nthawi yodziwika padziko lapansi. Chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah chakhanzikika kuchokera pa mahadith ambiri a swahiih a Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam).
Insha Allah, mu zigawo zikubwerazi, tikambirana za mahaadith omwe chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah chimakhanzikika.