Hazrat Abdullah bin Mas’uud (radhiyallahu ‘anhu) ndi Izindikiri wake a Quraan Majiid

Shaqiiq bin Salamah (rahimahullah), ophunzira wa Abdullah bin Mas’uud (radhiyallahu ‘anhu), akunena kuti nthawi ina yake, Abdullah bin Mas’uud (radhiyallahu ‘anhu) adapereka khutbah.

Mu khutbahmo adati, “Ndikulumbira qasam mwa Allah! Ndinaphinzira ma surah oposa makumi asanu ndi awiri a Quraan Kariim mwachindunji kuchokera kwa Rasulullah (sallallahu alaihi wasallam). Ndikulumbira m’dzina la Allah kuti ma Sahaabah (radhiyallahu ‘anhum) amadziwa kuti ndine m’modzi mwa odziwa bwino Quraan. Komano sindimadzitenga kuti ndiine opambana kwambiri mwa iwo.”

Malinga ndi zitabu zina, Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) ananenanso kuti, “Ndikanadziwa za munthu wina aliyense oidziwa Quraan Kariim), ndikanapita kwa iye kuti ndikaphunzire kwa iye.”

Shaqeeq bin Salamah (rahimahullah) anati, “(Pambuyo pa khutbah iyi), ndinapita ndikukhala m’misonkhano ya ma Swahaaba ena (radhiyallahu ‘anhum) kuti ndimvetsere zomwe anganene (Zokhudza khutbah ya Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu)). Sindinamvepo aliyense wa iwo akukana kapena kutsutsa zomwe adanena.” (Saheeh Bukhaariy #5000, Saheeh Muslim #2462, Fathul Baari 48/9)

Check Also

Kulimba Mtima kwa Hazrat Abdullah bin Mas’uud (Radhiyallahu ‘anhu)

Pankhondo ya Hunain, Asilamu adagonjetsedwa kwakanthawi kochepa. Munthawi yovutayi, Hazrat Abdullah bin Mas’uud (Radhwiyallahu ‘anhu) …