Tulo ndi chimodzi mwa zinthu zofunikira kwambiri kwa munthu aliyense, monga mmene kudya ndi kumwa zilili zofunikira kwambiri. Allah Talaa akutchula za ubwino waukulu wa tulo mu Qur’aan Majiid ponena kuti:
Ndipo tidakupangirani tulo kukhala mpumulo.
M’ndime ina Allah Talaa akuti:
Iye ndi Yemwe adakupangirani usiku kukhala chovala (chokuphimbani ndi mtendere ndi mpumulo), ndipo Walichita tulo kukhala njira yopumulira (kwa inu), ndipo Waupanga usana kukhala nthawi youka.
Pali ma sunnat ndi ma adaab osiyanasiyana okhudza kugona. Mkatikati mwa izi pali kuwerenga ma surah ndi masnoon dua ndi kugona ndi wudhu.
Munthu amene amawerenga ma surah ndi ma dua adzatetezedwa ku zoipa za ma shayaatuin ndipo adzapulumutsidwa ku maloto oipa. Ngati munthu wamwalira, ntchito yake yomaliza chidzakhala kukumbukira Allah ndipo adzadalitsidwa ndi ulemelero wa shahidi kudzera mu kugona ali ndi wudhu.
Pogona, munthu ayenera kupanga niya yoti akukwaniritsa izi kuti akhalenso ndi mpamvu kuti athe kukwaniritsa ibaadah ya Allah akadzuka. Chimodzimodzinso, akugona kuti akwaniritse ufulu wa thupi lake, monga popeza Allah adalipatsanso ufulu thupi lake.
Choncho, munthu akamachita ma sunnat awa asanagone, sadzangokwaniritsa kufunikira kwake kwa tulo – komanso adzakhala akupeza mphotho chifukwa tulo lake lidzakhala ngati ibaadah.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu