Kusamalitsa kwakukulu Kwa Sayyiduna Abdullah bin Mas’ood (radhiyallahu ‘anhu) Potulutsa mahadith a Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam)

Ole.wkezeka ‘Amr bin Maimoon (rahimahullah) adafotokoza za kusamalitsa kwakukulu kwa Abdullah bin Mas’ood (radhiyallahu ‘anhu) pamene ankatulutsa mahaadith kuchokera kwa Rasulullah (ssallallahu alaihi wasallam).

Adanena kuti, “Nthawi ina, Abdullah bin Mas’ood (radhiyallahu ‘anhu) atayamba kunena Hadith yochokera kwa Rasulullah (sallallahu alaihi wasallam), adagwidwa ndi mantha ndi nkhawa kotero kuti madontho a thukuta adawoneka pachipumi pake.

Atanena Hadith yo, adayankhula ndi anthu nati, ‘Izi ndi zomwe Rasulullah (sallallahu alaihi wasallam) adanena kapena kuforokoza zinazake zofananira ndi izi.’ (Al Mustadrak #5374)

Uku kudali kusamalitsa kwakukulu komwe Abdullah bin Mas’ood (radhiyallahu ‘anhu) ankaonetsa amafotokoza Mubaarak Ahaadith a Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam). Ankagwidwa ndi mantha ndi nkhawa kuti asalakwitse pofotokoza mawu a Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam), ndipo sayenera kulakwitsa kunena kuti china chake ndi chochokera kwa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) koma Iye sananene.

Chifukwa chomwe chinkapangitsa mantha ndi nkhawa chinali chakuti Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) adatchula mu Hadith yake yodalitsika, “Munthu amene wapeka china chake ndikuchikankhizila kwa ine, ameneyo akudzikonzera malo ake okhala kumoto wa Jahannum.” (Swahiyh Bukhaariy #107)

Check Also

Hazrat Abdullah ibn Mas’uud (radhiyallahu anhu) Kuwerenga Qur’aan Majeed mokweza mawu pamaso pa Aquraish

Hazrat Abdullah ibn Mas’uud (radhiyallahu anhu) adali munthu oyamba kuwerenga Qur’aan Majeed mokweza mawu ku …