Abdullah bin Maslamah Q’anabi (rahimahullah) anali m’gulu la ma Muhadditheen otsogola mu nthawi yake. Iye anali mtsogoleri wa ma Muhadditheen ambiri otchuka, ngati Imaam Bukhaari, Imaam Muslim ndi Imaam Abu Dawood (rahimahullah)
Zikunenedwa kuti pachiyambi cha moyo wake, ankacheza ndi anthu oipa ndipo ankamwa mowa.
Komabe, atakumana ndi Muhaddith wamkulu komanso oyera mtima, Imaam Shu’bah (rahimahullah) panali kusintha kwakukulu komwe kunalowa m’moyo wake ndipo anakhala m’gulu la anthu odalirika pa Chisilamu.
Pansipa pali nkhani yomwe inamupangitsa kulapa ndi kusintha:
Abdullah bin Maslamah nthawi ina anakhala pakhomo la nyumba yake, ali mkati modikira anzake kuti afike. Ali chikhalire, adaona Muhaddith wamkulu, Imaam Shu’bah (rahimahullah) akudutsa pafupi ndi nyumba yakeyi atakwera bulu wake.
Panali anthu ambiri omwe ankayenda m’mbali ndi kumbuyo kwa bulu wa Imaam Shu’bah (rahimahullah) ndi cholinga chofuna kupindula ndi mawu ake ndi kukhala naye.
Ataona Imaam Shubah (rahimahullah) ndi khamu lalikulu la anthu omwe adamuzungulira, Abdullah bin Maslamah adafunsa, “Kosi Munthu uyu ndi ndani?” Munthuyo adayankha nati: “Ndi Imaam shubah (rahimahullah).”
Abdullah bin Maslamah adafunsa kuti: “Kodi ntchito yake ndi yotani?” Bamboyo anayankha. “Iye ndi Muhadith (munthu amene amafotokoza Mahaadith a Mtumiki (SwallaAllaahualaihi wasallam).”
Atamva izi, Abdullah bin Maslamah yemwe panthawiyo adali atavala lungi (nsalu) yofiira, adayimilira ndikukakumana ndi Imaam Shu’bah (rahimahullah). Atafika kwa Imaam Shu’bah adayankhula naye modzidzimutsa ndikumuuza kuti: “Ndifotokozereko Hadith.”
Poona maonekedwe a Abdullah bin Maslamah, Imaam Shu’bah (rahimahullah) adazindikira kuti munthuyu ndi munthu osadzipereka ku Dini.
Choncho Imaam Shu’bah (rahimahullah) adayankha nati: “Ndingakufotokozere bwanji ma Hadith pomwe iwe siuli mgulu la omwe akuphunzira ma Hadith (sihnavale moyenera komanso siunakwaniritse miyambo yophunzilira Hadith ya Mtuiki (Swallallahu alaihi wasallam)?
Abdullah bun Maslamah atamva izi adakwiya kwambiri. Adatulutsa mpeni wake ndikumuopseza Imaam Shubah (rahimahullah) kuti “Undifotokozere Hadith pompano kapena ndikubaya!”
Imaam Shu’bah (rahimahullah) adayamba kufotokoza kuti: “Mansur akufotokoza kuchokera kwa Rib’i, yemwe akuforokoza kuchokera kwa Abu Masuud kuti Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam adati “Ngati ulibe khalidwe la hayaa (manyazi), chita zomwe ukufuna (popeza munthu akasowekera hayaa (manyazi), ndiye kuti samakhala ndi ulemu ndipo amakhala okonzeka kuchita tchimo lililonse).”
Imaam Shu’bah anali munthu wa olemekeza Sunnah za Rasulullah (sahallhu alyahi wasallam) ndi Chifukwa chake, pamene mawu awa adatuluka mumtima mwake, adakhudza kwambiri mtima wa Abdullah bin Maslamah kotero kuti nthawi yomweyo adagonja ndi chisoni ndipo adalapa moona mtima machimo ake.
Anaponya mpeni wake pansi, anabwerera kunyumba ndikutaya mowa wake onse.
Kenako anauza amayi ake kuti, “Anzanga abwera posachedwa, Akabwera aloreni alowe ndikuwapatsa chakudya. Akadya muwauze kuti ndasintha moyo wanga ndipo ndataya vinyo yense.”
Kenako adanyamuka ulendo opita ku Madina Munawwarah ndi cholinga chosintha moyo wake ndikukaphunzira Hadith pansi pa Imaam wamkulu wanthawiyo, Imaam Maalik (rahimahullah).
Adakhala ndi Imaam Maalik (rahimahullah) mpaka Allah Talaa adamdalitsa ndi chuma cha deen ndipo adakhala Imaam pa sayansi ya Hadith.
Kuchokera pa nkhaniyi, tikuphunzira kuti munthu aliyense sakuyenera kutaya chiyembekezo pa kusintha kwa munthu wina wake.
Panali anthu ambiri omwe ankakhala moyo wauchimo, koma kenako anadzilumikiza ndi abwenzi apadera a Allah ndipo anatembenukira kwa Allah Talaa kudzera mu kulapa moona mtima. Kenako anasintha miyoyo yawo kudzera mukukhala nawo limodzi.
Pambuyo pake, Allah Talaa anawadalitsa ndi kudzipereka ndi kuvomereza kotero kuti anakhala zitsanzo zabwino kwa anthu ammudzi kuti azitsatira.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu