Chifukwa Chimene Allah Adamudalitsira Abu Hurairah (radhiyallahu ‘anhu) Ndi Mpamvu Yokumbukira Mwachangu

Nthawi ina, Abu Hurairah (radhwiyallahu ‘anhu) adawayankhula anthu nati: ‎

Anthu inu mukunena kuti, “Bwanji Abu Hurairah akufotokoza Mahaadith ambiri kuchokera kwa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam), pomwe ma Swahaabah ena ngati ma Muhaajireen ndi Ansaaar sakunena mahaadith ochuluka choncho kuchokera kwa Rasulullah (Swallallahu ‎‎‘alaihi wasallam)?” ‎

Chifukwa chake n’chakuti nthawi ya Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam), abale anga ma Muhaajireen ankatanganidwa ndi kuchita malonda m’misika, pomwe ine ndinkakhala ndi Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam), ndikukhutira ndi chilichonse chomwe chingaloowe m’mimba mwanga. Ndinkakhalapo nthawi imene iwo kunalibe, ndipo tsopano ndikukumbukira Mahadith a Rasullalullah (Sallallahu ‎‘alaihi wasallam) omwe iwo adawaiwala.

Chimodzimodzinso, abale anga ma Ansaari ankatanganidwa ndi kusamalira minda yawo ya zipatso, pomwe ine ndinali munthu osauka omwe ndidali mgulu la ma Swahaaba osauka otchedwa Ashaabus Suffah (kutanthauza kukhala mu ‎musjid ya Rasulullah [Swallallahu ‘alaihi wasallam]). Tsopano ndikukumbukira mahadith a Rasullaullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) pomwe iwo adaiwala.

Abu Hurairah (radhwiyallahu ‘anhu) pambuyo pake adatchula chifukwa chomwe Allah Ta’ala adamudalitsira ndi nzeru zodabwitsa komanso chodabwitsa chomwe maSwahaaba ena sanapatsidwe. Iye akunena kuti:‎

Nthawi ina, Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) akufotokoza za Hadith, iye anauza omwe analipo pamalopo kuti, “Aliyense pakati panu amene ayale nsalu yake pansi pamaso panga, mpaka nditamaliza zomwe ndikunena, ndipo pambuyo pake atenga nsalu yake ndikufunda pa thupi lake, adzakumbukira zonse zomwe ndinganene (monga, adzakumbukira mahadith onse omwe angamve kwa ine ndipo sadzaziiwala).”

Abu Hurairah (radhwiyallahu ‘anhu) akunena kuti, “Nditamva izi kuchokera kwa Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam), nthawi yomweyo ndinatambasula nsalu yanga ndikuiyala pansi pamaso pa Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam), ndipo Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) atamaliza kufotokoza Hadith yake, nthawi yomweyo ndinatenga msalu yanga ndikuikulunga pa thupi langa ndi pachifuwa panga.” ‎

Kenako anati, “Kuyambira nthawi imeneyo, sindinaiwale chilichonse chimene ndinamva kuchokera kwa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam).” (Saheeh Bukhaari #2047, Saheeh Muslim ‎#2493)‎

Check Also

Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) Osafuna Kuchitidwa Opaleshoni ya Diso Chifukwa Chopereka Vuto ku Swalah Yake

Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) adadwala diso zomwe zidapangitsa kuti lidzitulutsa madzi nthawi zonse. Dokotala …