Ulemu wa Abu Hurairah (Radhwiyallahu ‘anhu) kwa Mdzukulu wa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) – Hasan (Radhiyallahu ‘anhu)

Said bin Abi Sa’eed Al-Maqburi (rahimahullah) akufotokoza izi:

Tsiku lina tidali limodzi ndi Abu Hurairah (Radhwiyallahu ‘anhu) pamene Hasan bin ‘Ali (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adadza kwa ife natilonjera ndi salaamu. Gulu lomwe lidamuzungulira Abu Hurairah (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adamumva akupereka salamu kwa iwo ndipo adamuyankha. Pambuyo pake, Hasan (Radhwiyallahu ‘anhu) atachoka pagululo napitiliza ulendo wake. Chifukwa chotanganidwa Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu ‘anhu) sadazindikire kuti Hasan (radhwiyallahu ‘anhu) wabwera kudzawapatsa salamu.

Munthu wina atamuuza kuti Hasan (radhwiyallahu ‘anhu) wabwera ku nkumanowo ndipo anawapatsa salamu kenako anachoka, iye (Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu ‘anhu)) anadzimvera chisoni kuti sanadziwe za kupezeka kwa Hasan (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo sanayankhe salamu yake.

Nthawi yomweyo anasuntha pa gulupo ndipo anapita kukamufunafuna Hasan (radhwiyallahu ‘anhu) kuti akayankhe salamu yake. Atamupeza anayankha salaam yake nati, “Wa ‘alaikas Salaam ya Sayyidi ( ntendere ukhale pa inu, O mtsogoleri wanga).”

Pambuyo pake munthu wina adamufunsa Abu Hurairah (radhwiyallahu ‘anhu), “N’chifukwa chiyani unamuitana Hasan (radhwiyallahu ‘anhu) dzina loti ‘Sayyidi’ (mtsogoleri wanga)?” ‎

Abu Hurairah (radhwiyallahu ‘anhu) anayankha kuti, “Chifukwa chomwe ndamuitanira dzina ili ndi chakuti ndinali limodzi ndi Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) pamene ndinamumva akumuitana Hasan (radhwiyallahu ‘anhu) ndi dzina ili. Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anati, “Ndi Sayyid (mtsogoleri wa ummah uwu).””‎ ‎(Majma’uz Zawaa’id #15049 ndi Mustadrak Haakim #4792)‎

Check Also

Kusamala pa Gwero la Munthu Wopeza Chidziwitso cha Deeni

Nthawi ina munthu wina dzina lake Bushair bin Ka’b al-Adawi adadzakumana ndi Abdullah bin Abbaas …