Maduwa aimitsidwa kufikira durood itawerengedwa

عن عمر بن الخطاب رضي الله عنه قال : إن الدعاء موقوف بين السماء والأرض لا يصعد منه شيء حتى تصلي على نبيك صلى الله عليه وسلم (سنن الترمذي،  الرقم: ٤٨٦)

Sayyiduna Umar (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, maduwa amatsakamira m’lengalenga. Samadutsa kupita kumwamba ngati durood siikutumizidwa kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) (palibe galantidi yoti duwayo ilandiridwa).

Sayyiduna Talha (radhiyallahu anhu) pa nkhondo ya Uhud

Sayyiduna Zubair bin Awwaam (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti pa nkhondo ya Uhud Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adaphatikiza zovala zake za pankhondo pa thupi lake zokwana ziwiri.

Mkatikati mwa nkhondo, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adafuna kuti akwele pa phiri komano sadakwanitse kutero ndipo adamupempha Sayyiduna Talha (radhiyallahu anhu) kuti akhale pansi ndipo kudzera mukuthandizidwa ndi iyeyu, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adakwera pa phiri, Sayyiduna Zubair (radhiyallahu anhu) akufotokokoza kuti adamunva Mtumiki sallallahu alaih wasallam akunena mawu oti, kwakakamizidwa kwa Talha (kuti akapeze nawo shafaa pa tsiku la Qiyaamah).

Pa nkhondo ya Uhud Sayyiduna Talha (radhiyallahu anhu) adatenga nawo gawo ndipo adamuteteza Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) molimbika, nthawi zonse masahabah akamakambirana nkhani ya nkhondo ya Uhud m’mene idayendera ankati “tsiku ili lidali la Talha (radhiyallahu anhu)” Sayyiduna Talha (radhiyallahu anhu) ankamutchinga Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) pogwiritsa ntchito thupi lake ngati chichango cha Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Adavulazidwa mabala odutsa 80 pa thupi lake, ngakhale zidali choncho sadamusiye Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), ngakhale kuti dzanja lake lidafa. (Musnad Abi Dawood Attayalisi, 6)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …