1. Njira yogwilira miswaak ili motere, Munthu ayenere ayike chala chachikulu ndi chaching´ono pansi pa miswaak ndipo zala zake zotsalazo ayike mbali yapamwamba pa Miswaak.[1] 2. Gwirani Miswaak ndi mkono wamanja ndipo yambani kutsuka mano kuyambira mbali yakumanja.[2] 3. Tsukani mano mopingasa ndipo lilime mulitsuke molitsatira (mulitali make), chimodzimodzinso, tsukani …
Read More »Ubwino ogwiritsa ntchito miswak
1. Kugwiritsa ntchito miswak kumaonjezera sawaabu za swalah ka 70.
Sayyiduna Aaishah radhiyallahu anha akunena kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, swalah imene yapempheledwa utagwiritsa ntchito miswak (popanga wudhu) ilindi sawaab zokwana 70 kuposa swalah yomwe yaswalidwa popanda kugwiritsa ntchito miswak.
Read More »Nthawi Zomwe Ndi Sunnah Kusambanthawi Zomwe Ndi Sunnah Kusamba
Pali nthawi zambiri zimene kusamba ndisunnah, zina mwa nthawizi ndi izi:
1.Tsiku la Jumua (lachisanu).
Sayyiduna Abullah bin Umar (radhwiyallahu anhuma) akunena kuti Mtumiki (Sallallahu alaih Wasallam) anati,” pamene wina mwainu akubwera ku swala ya Jumua (lachisanu) ayenera kusamba.”
Read More »Kasambidwe Ka Sunnah Gawo 5
Zokakamiza Posamba
Pali zinthu ziwiri zomwe ndizokakamizidwa kuchita ukamasamba,
1. Kupanga niya yosamba musanayambe kusambitsa thupi lanu.
2. Kuthira madzi thupi lonse.
Read More »Kasambidwe Ka Sunnah-Gawo 4
14. Onetsetsani kuti madzi akufika pena paliponse pathupi lanu, nthawi ina iliyonse mukadzithira madzi dzinyureni ndicholinga chofuna kuonetsetsa kuti madziwo alowa pakhungu lonse, ngakhale kutangotsala malo ochepetsetsa kwambiri osathiridwa madzi, kusamba (kwa fardh) sikudzatheka, pamene mukusambitsa thupi, sambitsani kutsogolo kwake kenako kumbuyo.
Read More »Kasambidwe Ka Sunnah-Gawo 3
9. Pangani wudhu onse.
Sayyidatuna Aaishah (radhiyallahu anha) akunena kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankati akamakasamba (kusamba kwa fardh) ankayamba ndikusamba m’manja asanalowetse manjawo m’madzi, kenaka ankatsuka malo obisika kenaka ankapanga wudhu ngati m’mene ankapangira(wudhu) akafuna kuswali.
Read More »Kasambidwe Ka Sunnah Gawo 2
5. Yambani ndi kuwerenga Bismillah mukamasamba, ndikupanga niya yoti mukuchotsa hadathil akbar (unve waukulu).
6. Sambitsani zikhatho zanu katatu.
Read More »Masunnah Ndi Aadaab (miyambo) Ya Pa Kusamba – Gawo 1
1. Yang’anani ku Qiblah (komwe timayang’ana tikamaswali) mukamasamba. ndibwino kuvala chovala kutchinga maliseche pamene mukusamba.
2. Sambirani malo omwe wina sangakuoneni. ndibwino kusamba mutaphimba maliseche anu. komano ngati wina ali malo omwe sangaonedwe ndimunthu wina (ngati kubafa) ngati wina akusamba maliseche, ndizoloredwa.
Read More »
Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo La chisanu Nchinayi
25. Ngati mbali iliyonse yachiwalo chomwe ndi fardh kusambitsa pamene mukupanga wudhu yasiidwa osasambitsa, wudhu udzakhala opelewera.
Sayyiduna Umar (radhwiyallahu anhu) akunena kuti munthu anapanga wudhu nasiya malo amodzi osasambitsa kuphanzi kwake mlingo wachikhadabu poyang’anitsitsa malo amenewo Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anamuuza iye kuti “pita ukamalizitse kupanga wudhu wako.”
Read More »
Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo La chisanu Nchitatu
21. Sisitani (kukhula/kutikita ndi dzanja lanu) ziwalo zanu mokwanilira pamene mukusambitsa ndicholinga choti madzi afike paliponse.
22. Ziwalo zonse ziyenera kutsukidwa china pambuyo pachinzake mosachedwetsa.
Read More »
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu