Hafs bin Khaalid (rahimahullah) akusimba kuti bambo wina wachikulire yemwe adafika kuchokera ku Mewsil adamuuza kuti ndidatsagana ndi Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) pa umodzi mwa maulendo ake. Pa nthawi ya ulendo. Pamene tinali malo otseguka, ouma, Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) ankafunika kusamba. Anatero kwa ine. “Ndibiseni (ndi nsalu kuti ndisambe).” Ndinamubisa motero, …
Read More »Kuyankha kuitana kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) Pambuyo pa nkhondo ya Uhud.
Nthawi ina bibi Aaisha (Radhwiya Allahu ‘anha) analankhula kwa mphwake (mwana wa mlongo wake) “Urwah (rahimahullah) kuti. “E, mwana wa mlongo wanga! Makolo ako onse (bambo ako ndi agogo ako aakazi), Zubair (Radhwiyallah “anhu) ndi Abu Bakr (radhwiyullahu ‘anhu), anali m’gulu la ma Swahaabah amene Allah Ta’ala adalankhula za iwo …
Read More »Olemekezeka Zubair (Radhwiya Allahu ‘anhu) Asolola Lupanga Lake Kuti Amutetezere Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam)
Olemekezeka Urwah bun Zubair (rahimahullah) akufotokoza motere Nthawi ina yake, Shaitaan anafalitsa mphekesera yabodza yoti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) wagwidwa ndi ma Kuffaar gawo la kumtunda kwa Makka Mukarramah. Atamva mphekesera imeneyi, Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu), yemwe panthawiyo anali ndi zaka khumi ndi ziwiri zokha, nthawi yomweyo adanyamuka, nadutsa mchigulugulu …
Read More »Ntchito yabwino yomwe Sa’d (radhiyallahu ‘anhu) adalandira nayo nkhani yabwino yokalowa Jannah
Olemekezeka Anas (radhwiya allaahu ‘anhu) anasimba kuti nthawi ina maSwahaabah (radhwiyallahu anhum) adakhala ndi Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wasallam) pamene adati: “M’kanthawi kochepa aonekera munthu wa ku Jannah pamaso panu.” Nthawi yomweyo, Sa’d (radhwiyallahu anhu) adatulukira atanyamula nsapato zake kudzanja lake lamanzere, ndevu zake zikuchucha madzi a wudhu. Tsiku lachiwiri …
Read More »Zotsutsa za Anthu Ena aku Kufah:
M’chaka cha 21 A.H, anthu ena aku Kufah adadza kwa Umar (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo adadandaula za Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) kuti sakumaswalitsa bwino. Nthawi imeneyo, Sa’d (radhwiyallahu anhu) adasankhidwa ndi Umar (radhwiyallahu ‘anhu) kukhala bwanamkubwa waku Kufah. Umar (radhwiyallahu anhu) adamuitana Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo atafika adalankhula naye mwaulemu nati: “E, …
Read More »Muvi Oyamba kulasa Mchisilamu
Olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) adali m’gulu la ma Swahaabah omwe Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawatumiza m’chaka choyamba cha Hijrah kuti akalimbane ndi gulu la ma Quraishi Paulendowu, Mtumiki (sawllallahu alaihi wasallam) adamusnkha Sa’ d (radhwiyallahu anhu) kukhala mtsogoleri wa gululi, Pa ulendowu maswahaaba (radhwiyallahu ‘anhum) adapita ku Rabigh komwe adakumana …
Read More »Magazi Oyamba Kukhetsedwa Chifukwa cha Chisilamu
Muhammad bin Ishaaq (rahimahullah) anati: Kumayambiriro kwa Chisilamu, ma Swahaabah a Mtumiki (Swallallaahu ‘alaihi wasallam) ankaswali mobisa. Iwo ankapita kuzigwa za Makka Mukarramah kukaswali kuti Swalaah yawo ikhale yobisika kwa osakhulupirira (ndi kuti apulumuke ku mazunzo a anthu osakhulupirira). Tsiku lina Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adali nawo pamodzi ndi gulu la …
Read More »kuwakonda ma Answaar
Aamir (rahimahullah) mwana wa Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu), akufotokoza motere: Nthawi ina ndinati kwa bambo anga: “O, bambo anga okondedwa! Ine ndikuona kuti inu mumasonyeza chikondi chowonjezera ndi ulemu kwa ma Answaar poyerekeza ndi anthu ena.” Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adandifunsa: “E, mwana wanga! Kodi siukusangalatsidwa ndi izi?” ndinayankha, “Ayi! Sindine okondwa. …
Read More »Ulosi wa Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) okhudza Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) Kugonjetsa Qaadisiyyah
Pa mwambo wa Hajjatul Wadaa, Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adadwala ku Makka Mukarramah ndipo ankaopa kuti amwalira. Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) atabwera kudzamuona, adayamba kulira. Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adamfunsa: “Bwanji ukulira?” Sa’d (Radhwiyallaahu ‘anhu) adayankha: “Ndikuopa kuti ndingamwalilire m’dziko limene ndidachita Hijrah, ndipo kudzera mu kumwalilira kuno, malipiro …
Read More »Kukhazikika kwa Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) pa Imaan
Abu “Uthmaan (rahimahullah) anasimba kuti Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adati: “Ndime iyi ya Qur’aan idavumbulutsidwa ponena za ine. وَوَصَّيْنَا الْإِنسَانَ بِوَالِدَيْهِ حُسْنًا ۖ وَإِن جَاهَدَاكَ لِتُشْرِكَ بِي مَا لَيْسَ لَكَ بِهِ عِلْمٌ فَلَا تُطِعْهُمَا Ife tamulamula munthu kuchitira zabwino makolo ake. Ndipo (makolo Anu osakhulupirira) Akakukakamizani kuti Mundiphatikize (ndi chipembedzo Changa) …
Read More »