Sahaabah

Kutengapo mbali pa Nkhondo ya Badr

Ismaa’eel bin Abi Khaalid akuti Bahiyy (Rahimahullah) adati: “Panali anthu apakavalo awiri okha omwe ankamenyana ndi adani pa nkhondo ya Badr. Wina adali Olemekezeka Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) yemwe ankalimbana ndi adani kudzanja lamanja, ndipo winayo adali Miqdaad bun Aswad (Radhwiyallahu ‘anhu), yemwe ankamenya nkhondo kumanzere. Hishaam bun Urwah akusimba kuti …

Read More »

Kusamalitsa pofotokoza Hadith yochokera kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam)

Abdullah bin Zubair (Radhwiya Allaahu ‘anhu) akuti nthawi ina adafunsa bambo ake (omwe ndi) Zubair radhwiyallahu ‘anhu kuti, “Bwanji simumafotokoza ma haadiith a Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam), monga momwe amachitira ma Swahaabah ena (Radhwiyallahu anhum)?” Olemekezeka Zubair (Radhwiya Allahu ‘anhu) anayankha kuti, “Sindinachokepo kumbali ya Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi …

Read More »

Kulandira dzina loti ‘Mthandizi Wapadera’ wa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)

Pankhondo ya Ahzaab, yomwe imadziwikanso kuti Nkhondo ya Khandaq (Nkhondo ya Ngalande), Asilamu adalandira uthenga kuti Banu Quraizah adaswa lonjezo lawo loti adzakhulupirika kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndipo adajoina adani. Kuti atsimikize zomwe zamvekazi, Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawafunsa ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) kuti: “Ndani andibweretsere nkhani za anthu …

Read More »

Mabala owapeza munjira ya Allah Ta’ala

Hafs bin Khaalid (rahimahullah) akusimba kuti bambo wina wachikulire yemwe adafika kuchokera ku Mewsil adamuuza kuti ndidatsagana ndi Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) pa umodzi mwa maulendo ake. Pa nthawi ya ulendo. Pamene tinali malo otseguka, ouma, Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) ankafunika kusamba. Anatero kwa ine. “Ndibiseni (ndi nsalu kuti ndisambe).” Ndinamubisa motero, …

Read More »

Olemekezeka Zubair (Radhwiya Allahu ‘anhu) Asolola Lupanga Lake Kuti Amutetezere Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam)

Olemekezeka Urwah bun Zubair (rahimahullah) akufotokoza motere Nthawi ina yake, Shaitaan anafalitsa mphekesera yabodza yoti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) wagwidwa ndi ma Kuffaar gawo la kumtunda kwa Makka Mukarramah. Atamva mphekesera imeneyi, Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu), yemwe panthawiyo anali ndi zaka khumi ndi ziwiri zokha, nthawi yomweyo adanyamuka, nadutsa mchigulugulu …

Read More »

Ntchito yabwino yomwe Sa’d (radhiyallahu ‘anhu) adalandira nayo nkhani yabwino yokalowa Jannah

Olemekezeka Anas (radhwiya allaahu ‘anhu) anasimba kuti nthawi ina maSwahaabah (radhwiyallahu anhum) adakhala ndi Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wasallam) pamene adati: “M’kanthawi kochepa aonekera munthu wa ku Jannah pamaso panu.” Nthawi yomweyo, Sa’d (radhwiyallahu anhu) adatulukira atanyamula nsapato zake kudzanja lake lamanzere, ndevu zake zikuchucha madzi a wudhu. Tsiku lachiwiri …

Read More »

Zotsutsa za Anthu Ena aku Kufah:

M’chaka cha 21 A.H, anthu ena aku Kufah adadza kwa Umar (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo adadandaula za Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) kuti sakumaswalitsa bwino. Nthawi imeneyo, Sa’d (radhwiyallahu anhu) adasankhidwa ndi Umar (radhwiyallahu ‘anhu) kukhala bwanamkubwa waku Kufah. Umar (radhwiyallahu anhu) adamuitana Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo atafika adalankhula naye mwaulemu nati: “E, …

Read More »

Muvi Oyamba kulasa Mchisilamu

Olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) adali m’gulu la ma Swahaabah omwe Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawatumiza m’chaka choyamba cha Hijrah kuti akalimbane ndi gulu la ma Quraishi Paulendowu, Mtumiki (sawllallahu alaihi wasallam) adamusnkha Sa’ d (radhwiyallahu anhu) kukhala mtsogoleri wa gululi, Pa ulendowu maswahaaba (radhwiyallahu ‘anhum) adapita ku Rabigh komwe adakumana …

Read More »

Magazi Oyamba Kukhetsedwa Chifukwa cha Chisilamu

Muhammad bin Ishaaq (rahimahullah) anati: Kumayambiriro kwa Chisilamu, ma Swahaabah a Mtumiki (Swallallaahu ‘alaihi wasallam) ankaswali mobisa. Iwo ankapita kuzigwa za Makka Mukarramah kukaswali kuti Swalaah yawo ikhale yobisika kwa osakhulupirira (ndi kuti apulumuke ku mazunzo a anthu osakhulupirira). Tsiku lina Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adali nawo pamodzi ndi gulu la …

Read More »