Sahaabah

Kulimba Mtima kwa olemekezeka Ali (radhiyallahu ‘anhu)

Pa nkhondo ya Uhud, Sayyiduna Ali (radhwiyallahu ‘anhu) adawonetsa kulimba mtima kwambiri polimbana ndi adaniwo. Choncho, iye yekha ndiye anali ndi udindo opha atsogoleri anayi a chiQuraishi, omwe mwa iwo anali Talhah bin Abi Talhah. Nkhondo itatha, adapereka lupanga lake kwa mkazi wake olemekezeka, Bibi Faatimah (radhwiyallahu ‘anha), kuti atsuke …

Read More »

Chikondi cha olemekezeka Ali (radhwiyallahu ‘anhu) pa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam)

Nthawi ina yake Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) analibe chakudya choti adye kotero adavutika ndi njala. ‘Ali (radhwiyallaahu ‘anhu) atamva kuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) akumva njala, nthawi yomweyo mtima wake unadzazidwa ndi nkhawa ndi malingaliro. Chimenecho chinali chikondi chake pa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) kuti sadapume bwino pomwe adadziwa kuti …

Read More »

Dua ya Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) kwa Ali (radhwiyallahu ‘anhu) potumiza ku Yemen

Ali (radhwiyallahu ‘anhu) akuti: Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adanditumiza monga bwanamkubwa wake ku Yemen. Ndisananyamuke ndidalankhula naye ndipo ndidati: “E, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Inu mukunditumiza kwa anthu akuluakulu kuposa ine. Kuonjezera apo, ine ndiine mwana, ndipo ndilibe kuzindikira kulikonse pa kaweruzidwe kamilandu. Atamva nkhawa zanga, Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) …

Read More »

Kugula Malo Oonjezera Musjid-ul-Haraam

Nthawi ina Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adapita kwa munthu wina ku Makkah Mukarramah ndipo anati kwa iye, “O wakuti-ndi-wakuti! Kodi ungandigulitseko nyumba yako, kuti ndiwonjezereko nzikiti mozungulira Ka’bah, ndipo mu mphotho ya ntchito yabwinoyi, ndikukutsimikizira kuti udzakhala ndi nyumba yachifumu ku Jannah (kuwonjezera pa ndalama za nyumba yomwe utapatsidwe)?” Munthuyo …

Read More »

Kukonzekera nkhondo ya Tabuuk

Abdur Rahmaan bun Khabbaab (radhwiyallah anhu) akufotokoza motere: Ndinalipo pamene Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ankawalimbikitsa ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) kuti akonzekeretse asilikali ndi kutenga nawo gawo pa ulendo wa Tabuuk. Nthawi imeneyo Uthmaan (radhwiya allahu ‘anhu) adayimilira nati: “Oh Mthenga wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Ine ndikupereka ngamila zana limodzi …

Read More »

Kukhudzika pa Nkhani ya Kuyankha Mafunso pa Tsiku Lomaliza

Nthawi ina yake “Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adalowa m’khola lake la ziweto ndipo adapeza kapolo wake akudyetsera ngamira. Atachiona chakudyacho Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) sadasangalatsidwe ndi mmene kapoloyo adachikonzera  kotero adapotokora khutu lake. Patangopita nthawi pang’ono, atalingalira zomwe wachita, ‘Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adada nkhawa ndikuopa kuti sangamutsegulire mlandu pa zimene wachita tsiku …

Read More »

Makhalidwe khumi apadera a Uthmaan (radhwiyallahu anhu)

Hazrat Abu Thawr (rahimahullah) akuti tsiku lina adadza kwa Uthmaan (radhwiyallah”anhu) ndipo adamumva akunena izi panthawi yomwe adaukiridwa. Adati: “Pali ntchito zabwino zokwana khumi zomwe ndadziteteza kwa Allah Taala, ndipo pa ntchito iliyonse ndikuyembekeza kudzalandira malipiro pa tsiku lomaliza; 1) Ndinali munthu wachinayi kuvomereza Chisilamu. 2) Sindinanenepo bodza moyo wanga …

Read More »

Mantha a Hazrat Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) kuliopa tsiku lachiweruzo

Sayyiduna Haani (rahimahullah), kapolo womasulidwa wa Sayyiduna “Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu), akunena kuti: Hazrat ‘Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) ankati akayima pamanda, ankalira kwambiri moti ndevu zake zinkanyowa ndi misozi yake. Wina adamufunsa kuti: “Timakuwona kuti ukakumbukira Jannah ndi Jahanmum kapena kukambidwa  za izo, siumakhudzidwa kwambiri mpaka kuyamba kulira, pomwe ukayima pamanda timakuona …

Read More »

Kutsatira Njira Yofewa ndi Yodekha Pochita zinthu ndi Anthu:

“Ataa bin Farrookh (rahimahullah) akufotokoza motere: Tsiku lina lake ‘Uthmaan (radhwiyallaahu ‘anhu) adagula malo kwa munthu wina. Atagula malowa ‘Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adadikira kuti munthuyo adzatenge ndalama zake. Komabe, munthuyo sanabwere. ‘Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) adakumana ndi munthuyo pambuyo pake ndipo adamufunsa: “Bwanji sunabwere kudzatenga ndalama zako?” Bamboyo anayankha. “Chomwe chinandipangitsa …

Read More »

Hayaa ya Hazrat ‘Uthmaan (Radhiyallahu ‘anhu)

Hazrat Aaishah (radhiya allahu ‘anha) akusimba motere: Nthawi ina, Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) anali atagona kunyumba kwanga ndipo thupi lake linasunthidwa pang’ono kuchokera kudera la ntchafu zake zodalitsika kapena ntchafu yake yodalitsika, ngakhale ntchafu zodalitsidwa ndi shins zidakutidwa ndi lungi lake. Panthawi imeneyo, Abu Bakr (radhiyallahu ‘anhu) …

Read More »