Kuwolowa kwambiri manja kwa Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu)

Mkazi wa Talhah (Radhwiyallahu ‘anha), Su’da bint ‘Awf al-Muriyyah anakambapo izi zokhudza mwamuna wake Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu):

“Tsiku lina Talha analowa m’nyumba ali okhumudwa. Chavuta ndi chiyani? Kodi ndalakwitsa penapake mchifukwa ndikuwona kuti mukuonetsa kukhumudwa? Chonde ndiuzeni kuti ndithe kuchotsa kukhumudwa kwanu.

Iye adayankha, “Ayi, siunandilakwire chilichonse, ndipo ndithudi, ndiwe bwenzi labwino kwambiri pa moyo kwa munthu msilamu ngati ine.

Kenako ndinam’funsa kuti, ‘Ndifotokozereni vuto limene likukudetsani nkhawa.

Adandiuza: “Chuma chomwe ndili nacho chachuluka ndipo izi zikundisowetsa mtendere kwambiri.

Kenako ndinamutonthoza n’kunena kuti: “Palibe chifukwa choti udere nkhawa, bwanji osachigawa kwa anthu osauka.

Kenako Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu) adayamba kugawa kwa anthu osauka mpaka palibe dirham ngakhale imodzi yomwe idatsala.”

Talhah ibn Yahya (Rahimahullah) adanena kuti, “Ndinafunsa msungichuma wa Talhah (radhiyallahu ‘anhu), ‘Kodi Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu) adagawa chuma chochuluka bwanji panthawiyo?” Adati: “Iye adagawa ma dirham zikwi mazana anayi (400,000) kwa osauka pa nthawiyo.” (Hilyatul Awliyaa 1/88).

Check Also

Olemekezeka Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu pa Nkhondo ya Uhud

Pankhani ya kupirira kwa Talha (Radhwiyallahu ‘anhu) pankhondo ya Uhud, Sa’d bin Abi Waqqaas (Radhwiyallahu …