Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adampatsa olemekezeka Talhah (radhwiyallahu ‘anhu) dzina loti Al-Fayyaadh (munthu owolowa manja kwambiri) kangapo. Pansipa pali nkhani imodzi yotere:
Pankhondo ya Zi Qarad, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adadutsa pachitsime cha Baisaan. Madzi a m’chitsimechi ankadziwika kuti ndi anchere. Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati: “Chitsimechi chiyenera kutchedwa Na’maan kutanthauza madzi okoma.
Olemekezeka Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu) adagula chitsimechi kwa eni ake ndipo adachipereka asilamu kuti chiwapindulire. M’nkhani ina zikunenedwa kuti pankhondoyi, adaphanso ngamira ndikuwapatsa anthu nyama yake kuti adye. Tsiku limenelo Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati kwa iye: “E, Talhah! Ndithu, iwe ndiwe Fayyaadh (munthu owolowa manja kwambiri).