Bambo ake a Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) atalowa Chisilamu. Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) adalankhula kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) kuti: “Ndikulumbirira amene anakuikani m’choonadi! Ngakhale ndiri mchisangalaro kuti bambo anga alowa chisilamu, ndikadakhala osangalala kwambiri zikanakhala kuti omwe alowa chisilamu ndi amalume anu Abu …
Read More »Olemekezeka Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) amutumikira Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)
Hazrat Abu Bakr Siddeeq (Radhwiyallaahu ‘anhu) akusimba motere za ulendo wa Hijrah ndi Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam): Tinayenda mofulumira usiku wonse ndi gawo lina la tsiku lotsatira mpaka kutentha kwamasana kunakula kwambiri. Kenako ndinapeza kuti mseu mulibe munthu aliyense woyendamo. Ndinayang’ana kutsogolo kuti ndione ngati ndingapeze mthunzi uliwonse kuti tibisalemo. …
Read More »Ulemu wa Hazrat Abu Bakr (Radhiyallahu ‘anhu) kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ndi chikondi cha Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) pa Iye
Pa nthawi ya Fat-he-Makkah Mukarramah (Kugonjetsa Makka Mukarramah), Hazrat Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) adabweretsa bambo ake, Abu Quhaafah, kwa Rasulullah kuti akalowe Chisilamu. Pa nthawiyo Abu Quhaafah adali ndi zaka zoposa 90 zakubadwa ndipo adali atasiya kuona. Atadza kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam), Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamuuza Hazrat Abu …
Read More »Munthu Wabwino Kwambiri pa Ummah uwu
Hazrat Abu Dardaa radhiyallah anhu wanena kuti: “Nthaŵi ina yake, Mtumiki (Swallallaahu alaih wasallam). adandiona ndikuyenda kutsogolo kwa Hazrat Abu Bakr (Radhiyallahu ‘anhu) “Pamene Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adaona izi, adandiuza kuti: “Usayende kutsogolo kwa amene ali wabwino kuposa iwe. Pambuyo pake Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi …
Read More »Hazrat Abu Bakr Siddeeq (Radhwiyallahu ‘anhu) ali m’phanga la Thaur
Ali kuphangako paulendo wa Hijrah, zikunenedwa kuti Hazrat Abu Bakr Siddeeq (radhwiyallahu anhu) adali ndi nkhawa kuti palibe cholengedwa chomwe chingatuluke mu dzenje lililonse la mphangamo ndi kuvulaza Hazrat Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam). Choncho, anayamba kutseka mabowo onse a m’phangamo ndi zidutswa za malaya ake apansi. Komabe, padali mabowo awiri …
Read More »Olemekezeka Abu Bakr (Radhwiyallahu anhu) Kupereka Chuma Chake Kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)
Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallah alayhi wasallam) adati: “Palibe chuma cha munthu chomwe chidandipindulira monga chuma cha Abu Bakr (radhiyallahu anhu), atamva izi olemekezeka Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) adayamba kulira nati: “Chuma changa ndi zonse ndi zanu. Pali nkhani ya olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) m’buku …
Read More »Chikondi cha Hazrat Anas bin Nadhr pa Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) Kuphedwa ku Uhud
Pamene Asilamu adagonjetsedwa ku Uhud, mphekesera zidayamba kufalikira kuti Sayyiduna Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) waphedwa. Nkhaniyi idawapangitsa ambiri mwa ma Swahaabah kutaya mtima ndi kutaya chiyembekezo. Sayyiduna Anas bun Nadhr adawona Hazrat Umar ndi Hazrat Talhah pamodzi ndi gulu la ma Sahaabah ali mu chisoni chachikulu ndi kutaya mtima. Iye …
Read More »Answaari wina agwetsa nyumba pansi
Tsiku liina Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) ankadutsa mumsewu wa Madinah Munawwarah pamene adawona nyumba yomwe inali ndi dome. Adafunsa kwa Swahaabah. “Ichi ndi chiyani?” Anamuuza kuti inali nyumba yatsopano yomangidwa ndi mmodzi wa ma Ansaar. Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) anakhala chete. Tsiku lina, Answaari amene adamanga nyumbayo adadza …
Read More »Hazrat Bilaal (Radhiya Allaahu ‘anhu) pa imfa yake
Pamene Hazrat Bilaal (Radhiya Allaahu ‘anhu) adatsala pang’ono kumwalira, mkazi wake adayamba kunena kuti: “Ha! Ndi zomvetsa chisoni bwanji! Mukuchoka m’dziko lino!” Hazrat Bilaal (Radhiya Allahu anhu) anayankha kuti: “Zili zokondweretsa ndi zosangalatsa kuti mawa tikukakumana ndi abwenzi athu, tikakumana ndi Muhammad (Swalla Allaahu ‘alayhi wa sallam) ndi maswahaba ake.”
Read More »Nsembe ya maswahabah radhwiyallahu anhum pa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam)
Nyumba ya Bibi Faatimah (radhiyallahu anha) idali potalikirako ndi nyumba ya Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Tsiku lina Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamuuza kuti “khumbo langa ndiloti udzikhala nane pafupi” Bibi Faatimah (radhiyallahu anha) adayankha nati, Nyumba ya Haarithah ili pafupi ndi yanu, ngati mungamupemphe kuti tisinthanitse ndi yanga adzavomera mwansangala. …
Read More »