Yearly Archives: 2022

Chikondi cha Hazrat Uthmaan (radhiyallahu anhu) pa Hazrat Rasulullah (sallallahu alaih wasallam)

  Nthawi ya Hudaybiyah, Hazrat Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) adatumidwa ndi Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) kukakambirana ndi ma Quraish ku Makka Mukarramah. Pamene Hazrat Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) adanyamuka kupita ku Makka Mukarramah, ena mwa maswahabah adamchitira kaduka Uthmaan (radhiyallahu anhu) chifukwa chokwanitsa kuchita tawaaf ya nyumba ya Allah (ka’bah). Komano mthenga …

Read More »

Masunnah Ochita Mumzikiti

20. Osaimika swalah mumzikiti pa malo amene ungawatchingire anthu ena kudutsa mwaufulu. Mwachitsanzo kupemphera swalah pamalo polowera zimene zingapangitse ena kuti asadutse.

Olemekezeka Ibn Umar (radhiyallahu anhuma) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alayhi wasallama) adaletsa kupemphera swalah malo okwana asanu ndi awiri (ndipo amodzi mwamalowo) ndimalo odutsapo anthu.

Read More »

Chikondi chakuya  komanso chikumbutso cha Umar (radhwiyallahu anhu pa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam)

Usiku wina olemekezeka Umar (radhwiyallahu anhu) mu ulamuliro wake ali mkati moyendayenda kupereka chitetezo adaona kuwala kuchokera nyumba inayake komanso adamva mawu. Atapita komweko adapeza mayi wachikulire akuluka uku akulakatula ndakatulo iyi, عَلَى مُحَمَّدٍ صَلَاةُ الْأَبْرَارْ ** صَلَّى عَلَيْكَ الْمُصْطَفَوْنَ الْأَخْيَارْ Ndikuppha anthu onse olungama kuti apitirize kumfunira zabwino Mtumiki …

Read More »

Tafseer Ya Surah Asr

Ndikulumbilira nthawi; ndithudi munthu ndioluza, kupatula amene akhulupilira namagwira ntchito zabwino ndipo amalimbikitsana wina ndimnzake kutsatira choonadi komanso namalimbikitsana kupilira (komanso kupewa uchimo)

Read More »

Masunnah Ochita Mumzikiti

17. Osakangana ndiwina aliyense mumzikiti kumeneko ndikuonetsera kunyoza malo olemekezeka amzikiti.[1] 18. Ndipo ndizabwino kwambiri kuti musaupange mnzikiti kukhala njira yanu yodutsira popita tsidya lina.[2] عن ابن عمر رضي الله عنهما عن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال خصال لا تنبغي في المسجد لا يتخذ طريقا ولا يشهر فيه سلاح …

Read More »

Chikondi Cha Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) Kumukonda Nabi (sallallahu alaih wasallam)

Nabi (sallallahu alaih wasallam) adawuyamba nsamuko pamodzi ndi Abu Bakr (radhwiyallahu) anhu chakumadzulo, nkatikati mwa ulendowu, nthawi zina Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) ankayenda kutsogolo kwa Nabi (sallallahu alaih wasallam), ndipo nthawi zina ankayenda kumbuyo kwake, nthawi zina kumanja kwake ndipo nthawi zina kumanzere kwake. Nabi (sallallahu alaih wasallam) atazindikira machitidwe …

Read More »

Kuchulukitsa kuwerenga Duruud tsiku la Jumuah

Aws bin Aws (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adati tsiku labwino kwabwino kwambiri ndi tsiku la Jumuah (lachisanu) kotero Chulukitsani kundiwerengera duruud tsiku limeneli chifukwa duruud yanu imandifika, swahabah wina adafunsa nati Oh Mthenga wa Allah Duruud yathu idzakufikani bwanji mukadzamwalira ndipo mafupa anu adzakhala awola? Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adayankha nati, "ndithudi Allah Tabaaraka wata’ala adailetsa nthaka kudya matupi a aneneri alaihim salaam ."

Read More »

Masunnah Ochita Mumzikiti

14. Onesetsani kuti mwathimisa foni yanu pamene mukulowa mumzikiti ndicholinga choti musasokoneze nayo anthu amene ali otangwanika ndimapemphero ndi ma ibaada ena ndi ena.[1] 15. Osajambula mafoto kapena kupanga vidiyo pamene muli mumzikiti. Kujambula foto komanso kupanga vidiyo chinthu chamoyo ndi Haraam mchisilamu. ndipo kuchita zimenezi mumzikiti nditchimo lalikulu. عن …

Read More »