4. Werengani Surah Yaasiin m’mawa ndi madzulo aliwonse. Ibnu Abbaas (Radhwiyallahu anhu) adati: “Amene angawerenge Surah Yaasiin m’bandakucha, ntchito yake ya tsiku lonse idzafewetsedwa, ndipo amene angaiwerenge madzulo, ntchito yake mpaka m’mawa idzafewetsedwa.”[1] Olemekezeka Jundub (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anati: “Amene angawerenge Surah Yaasiin usiku ndi …
Read More »Monthly Archives: May 2024
Mabala owapeza munjira ya Allah Ta’ala
Hafs bin Khaalid (rahimahullah) akusimba kuti bambo wina wachikulire yemwe adafika kuchokera ku Mewsil adamuuza kuti ndidatsagana ndi Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) pa umodzi mwa maulendo ake. Pa nthawi ya ulendo. Pamene tinali malo otseguka, ouma, Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) ankafunika kusamba. Anatero kwa ine. “Ndibiseni (ndi nsalu kuti ndisambe).” Ndinamubisa motero, …
Read More »Swalaah Ndi Kiyi Yaku Jannah
Chisilam ndi njira yokhayo imene imamutsogolera munthu ku chikondi cha Allah Ta’ala komanso chimamutsogolera Jannah. kudzera mukutsatira machitidwe a chisilamu, Munthu adzapeza chisangalaro cha Allah Ta’ala komanso adzapedza chipambano chosatha. Muntchito zokakamizidwa zonse mchisilamu, swalah ndi imene ili pamwamba kwambiri pachikakamizo, Mtumiki wa Allah (Swallallah alayhi wasallam) adati; “Swalah ndi …
Read More »Surah Zokhala ndi nthawi zake zowerenga komanso nthawi zake zosiyanasiyana zomwe zikuyenera kuwerenga
Pali Surah zina zomwe zalamuridwa kuti ziziwerengedwa nthawi yodziwika usiku ndi usana kapena masiku ena a sabata. Ndi mustahab kwa munthu kuwerenga ma surah amenewa mu nthawi yake yoikidwa. 1. Werengani Surah Kaafiroon musanagone. Olemekezeka Jabalah bun Haarithah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallah alaihi wasallam) adati: “Ukamakagona, werenga Surah …
Read More »Kuyankha kuitana kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) Pambuyo pa nkhondo ya Uhud.
Nthawi ina bibi Aaisha (Radhwiya Allahu ‘anha) analankhula kwa mphwake (mwana wa mlongo wake) “Urwah (rahimahullah) kuti. “E, mwana wa mlongo wanga! Makolo ako onse (bambo ako ndi agogo ako aakazi), Zubair (Radhwiyallah “anhu) ndi Abu Bakr (radhwiyullahu ‘anhu), anali m’gulu la ma Swahaabah amene Allah Ta’ala adalankhula za iwo …
Read More »Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 10
23. Ngati mudaloweza pamtima gawo lina lake la Qur’an Majiid, onetsetsani kuti mukulibwereza nthawi zonse kuti musaiwale. Hadith yachenjeza za kunyalanyaza kuwerenga Quraan ndi kuiwala zomwe waloweza pamtima.[1] Olemekezeka Abu Musah Ash’ari (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah Adati: “Isamareni Qur’an Majiid. Ndikulumbirira Amene m’manja Mwake muli moyo wanga, (Qur’an Majiid) …
Read More »Olemekezeka Zubair (Radhwiya Allahu ‘anhu) Asolola Lupanga Lake Kuti Amutetezere Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam)
Olemekezeka Urwah bun Zubair (rahimahullah) akufotokoza motere Nthawi ina yake, Shaitaan anafalitsa mphekesera yabodza yoti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) wagwidwa ndi ma Kuffaar gawo la kumtunda kwa Makka Mukarramah. Atamva mphekesera imeneyi, Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu), yemwe panthawiyo anali ndi zaka khumi ndi ziwiri zokha, nthawi yomweyo adanyamuka, nadutsa mchigulugulu …
Read More »Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 9
21. Mukamaliza kuwerenga Qur’an yonse mpaka kukafika Surah Naas, zili mustahab kuti muyambirenso kuwerenga poyambiranso ndi Surah Faatihah ndi aya zoyambira za Surah Baqarah mpaka ulaaika humul muflihuun. 22. Mukamaliza kuwerenga Quraan yonse, werengani dua iyi: اَللّٰهُمَّ ارْحَمْنِيْ بِالْقُرْآنْ وَاجْعَلْهُ لِيْ إِمَاماً وَّهُدًى وَّرَحْمَةً اَللّٰهُمَّ ذَكِّرْنِيْ مِنْهُ مَا نَسِيْتُ وَعَلِّمْنِيْ …
Read More »Ntchito yabwino yomwe Sa’d (radhiyallahu ‘anhu) adalandira nayo nkhani yabwino yokalowa Jannah
Olemekezeka Anas (radhwiya allaahu ‘anhu) anasimba kuti nthawi ina maSwahaabah (radhwiyallahu anhum) adakhala ndi Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wasallam) pamene adati: “M’kanthawi kochepa aonekera munthu wa ku Jannah pamaso panu.” Nthawi yomweyo, Sa’d (radhwiyallahu anhu) adatulukira atanyamula nsapato zake kudzanja lake lamanzere, ndevu zake zikuchucha madzi a wudhu. Tsiku lachiwiri …
Read More »