Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 8

20. Musatemberere ana anu pamene mukupempha pa Swalah kapena nthawi ina iliyonse. Ndizotheka kuti temberero lanu litha kukumana ndi nthawi yomwe ma dua amayankhidwa.

Olemekezeka Jaabir (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Musadzitemberere nokha, ana anu, akapolo anu, kapena chuma chanu.Temberero lanu likhoza kukumana ndi nthawi (yoyankhidwa) pamene chilichonse chikapemphedwa kwa Allah chipatsidwa.”[1]

21. Musakhale pa changu ndi kusapilira kuti duwa yanu iyankhidwe ndi kukwaniritsidwa.

Olemekezeka Anas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Kapolo adzakhalabe muubwino pamene ali (kukondwera ndi lamulo la Allah) ndipo Sali pa changu.” Swahaabah adafunsa kuti: “E, Nabiy wa Allah! Kodi kuchita zinthu mopupuluma kukutanthauza chiyani?” Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “kunena kuti: “Ndidapempha kwa Mbuye wanga, koma sadandiyankhe duwa yanga.”[2]

22. Ngati munthu akuona kuti ma dua ake sakuyankhidwa, asataye chiyembekezo koma apitirize kumupempha Allah. Azindikire kuti Allah akudziwa chomwe chili chabwino kwa kapolo aliyense ndipo Allah adzachipereka kwa kapoloyo pa nthawi yoyenera.

Olemekezeka Abu Sa’iid Khudri (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Msilamu aliyense amene wapemphera kwa Allah ndi kum’pempha, ndipo duwa yake ilibe tchimo lililonse (monga kupempha chinthu choletsedwa) kapena kuthetsa ubale wakubanja. , Allah adzampatsa chimodzi mwa zinthu zitatu. nkutheka adzampatsa zimene wapempha (padziko lapansi), kapena Adzamsungira malipiro a duwa ku Aakhirah, kapena adzamuchotsera tsoka.” Swahaabah wina adati: “Ngati ndi choncho, tidzichulukitsa ma dua ambiri.” Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anayankha kuti: “Allah ndi oposa chilichonse (ndi mphamvu zake ndi nkhokwe zake nzoposa zimene mukuzipempha).[3]


[1]سنن أبي داود، الرقم: 1534، وقال العلامة المنذري رحمه الله مختصره 1/443: وأخرجه مسلم في أثناء حديث جابر الطويل

[2] مسند أحمد، الرقم: 13008، وقال العلامة المنذري رحمه الله في الترغيب والترهيب، الرقم: 2552: رواه أحمد واللفظ له وأبو يعلى ورواتها محتج بهم في الصحيح إلا أبا هلال الراسبي

[3] مسند أحمد، الرقم: 11133، وقال العلامة الهيثمي رحمه الله في مجمع الزوائد، الرقم: 17210: رواه أحمد وأبو يعلى بنحوه والبزار والطبراني في الأوسط ورجال أحمد وأبي يعلى وأحد إسنادي البزار رجاله رجال الصحيح غير علي بن علي الرفاعي وهو ثقة

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 6

16.Lekani kulongosora mwatsatanetsatane pa dua yanu. M’malo mwake, muyenera kupempha zabwino zonse. Nthawi ina Abdullah …