Kuyendera Odwala

Chipembedzo cha Chisilamu chimalimbikitsa ndi kulamula kuti munthu akwaniritse udindo umene ali nawo kwa Allah ndi udindo umene ali nawo kwa akapolo a Allah. Pankhani ya udindo ndi maufulu omwe munthu ali nawo pa akapolo a Allah, izi zikhoza kugawidwa m’mitundu iwiri ya maufulu.

Mtundu oyamba ndi ufulu umene uli olunjika kwa munthu aliyense payekha payekha. Mwachitsanzo; ufulu umene munthu ali nawo kwa makolo ake, abale ake, anansi ake, ndi ena otero.

Mtundu wachiwiri ndi ufulu umene umakhudza Asilamu onse. Pankhani ya mtundu uwu, Rasulullah swallallahu alaihi wasallam wafotokoza mu Hadith yake yolemekezeka kuti Msilamu aliyense ali ndi maufulu asanu ndi umodzi pa Asilamu anzake. Mwa maufulu asanu ndi Umodziwa ndi wakuti munthu apite kukamuyendera msilamu nzake akadwala.

Olemekezeka Ali (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) anati, “Msilamu ali ndi maufulu asanu ndi umodzi pa Msilamu nzake. akakumana naye, amlonjere (ndi salaam); ngati amuitana, avomere kuitana kwake; akayetsemula (ndi kunena kuti alhamdulillah), ayankhe kuyetsemula kwake ponena kuti ‘Yarhamukallah’; akadwala, azipita kukamuona, Akamwalira apite ku maliro ake; ndipo azimukonda ngati mmene amazikondera iye mwini.”