Ubwino Oyendera Odwala 1

Kupeza Mwayi Opangiridwa Dua Ndi Angelo Okwana Zikwi Makumi Asanu Ndi Awiri (70,000) 

Olemekezeka Ali (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene amayendera odwala m’bandakucha, angero zikwi makumi asanu ndi awiri (70,000) amamupemphera chifundo kwa Allah mpaka madzulo; Amene angamuyendere odwala madzulo angelo okwana 70,000 amamupemphera chifundo kwa Allah mpaka kucha, ndipo adzalandira Munda wa mtendere.” [1]

Kumanga Nyumba Yachifumu ku Jannah

Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene angayendere munthu odwala, mngelo amamuitana kuchokera kumwamba kuti: ‘Khala mwabata ndi mtendere. Kukongolerenji kuyenda kwako (kukakumana ndi m’silamu nzako ndi kukamuonetsera kukhudzika kwako) ndi (kudzera mukuchita zimenezi), wadzimangira nyumba yachifumu ku Jannah.’” [2]

Kupeza Chisangalalo cha Allah

Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alahi wasallam) adati: “Pa tsiku la Qiyaamah, Allah adzati, ‘E iwe mwana wa Adam! Ndinadwala koma iwe siunadzandione.’ Munthuyo adzayankha kuti, ‘E inu Allah, zikadatheka bwanji kuti ndidzakuoneni pamene Inu mwadwala pamene Inu ndinu Mbuye wa zolengedwa? (i.e. Inu simuli ngati anthu amene amadwala).’ Allah adzayankha kuti: ‘Kodi siukudziwa kuti kapolo Wanga wakuti wakuti adadwala, ndipo iwe siunakamuone? Kodi sukudziwa kuti ukadamuyendera, ukadandipeza’”[3]


[1] سنن الترمذي، الرقم: 969، وقال هذا حديث حسن غريب

[2] سنن ابن ماجة، الرقم: 1443، سنن الترمذي، الرقم: 2008، وقال: هذا حديث غريب

[3] صحيح مسلم، الرقم: 2569

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 7

18. Popempha mpempheni Mulungu kuti akudalitseni ndi aafiyah (ie kuti akudalitseni momasuka m’magawo onse a …