Ubwino Oyendera Odwala 2

Kutalikitsidwa ndi Jahannam kwa ntunda okwana kuyenda zaka makumi asanu ndi awiri (70)

Olemekezeka Anas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene wapanga wudhu olongosoka (pokwaniritsa masunnah ndi ma mustahabbaat) ndi kupita kukamuona m’silamu nzake yemwe akudwala ndi chiyembekezo choti adzalandire malipiro okayendera nsilamu odwala, munthu oteroyo adzaikidwa kutali ndi Jahannam kwa ntunda okwana kuyenda zaka makumi asanu ndi awiri (70).”

Kukhala M’munda wa Jannah

Olemekezeka Thawbaan (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene angakayendere m’bale wake wa Chisilamu (amene akudwala) amakhala m’munda wa Jannah (kuyambira pamene wanyamuka) mpaka kubwerako.”

Kukutidwa ndi Chifundo cha Allah

Olemekezeka Jaabir (Radhwiyallah anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallah alaihi wasallam) adati: “Munthu akapita kukayendera odwala amalowa mu rahmah (chifundo) ya Allah. Pambuyo pake akakhala ndi odwala, amakhala okutidwa kwathunthu mu rahmah (chifundo) ya Allah.”

Khalidwe la anthu aku Jannah

Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) anasimba kuti nthawi ina, Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adafunsa kuchokera kwa ma Swahaabah kuti: “Ndani mwa inu amene akusala kudya lero?” Abu Bakr (Radhwiyallahu anhu) anayankha kuti: “Lero ine ndikusala kudya.” Kenako Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adafunsa: “Ndani mwa inu amene wayendera odwala lero?” Abu Bakr (Radhwiyallahu anhu) anayankha kuti: “Lero ndamuyendera munthu odwala.” Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adafunsanso kuti, “Ndani mwa inu lero waswalira nawo Jeneezah?” Abu Bakr (Radhwiyallahu anhu) anayankha kuti: “Lero ndaswalira nawo Jeneezah.” Kenako Rasulullah (Radhwiyallahu anhu) adafunsa: “Ndani mwa inu lero wadyetsa osauka? Abu Bakr (Radhwiyallahu anhu) anayankha: “Lero ndadyetsa munthu osauka. Pambuyo pake, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Ndithu amene ali ndi makhalidwe onsewa adzalowa ku Jannah.”[4]


[1] سنن الترمذي، الرقم: 2736، وقال: هذا حديث حسن

[2] صحيح مسلم، الرقم: 2568

[3] عن جابر بن عبد الله، قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من عاد مريضا لم يزل يخوض الرحمة حتى يجلس، فإذا جلس اغتمس فيها هذا حديث صحيح على شرط مسلم، ولم يخرجاه (المستدرك على الصحيحين للحاكم، الرقم: 1295، وقال العلامة الهيثمي – رحمه الله – في مجمع الزوائد 2/297: رواه أحمد والبزار ورجال أحمد رجال الصحيح

[4] صحيح مسلم، الرقم: 1028

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 7

18. Popempha mpempheni Mulungu kuti akudalitseni ndi aafiyah (ie kuti akudalitseni momasuka m’magawo onse a …