Ammaar bin Yaasir (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adati: “Allah Ta’ala adasankha Mngelo oti akhale pambali pa manda a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), Mngelo amene Allah adampatsa nzeru zodziwa maina (mu hadith ina zanenedwa kuti adapatsidwa kuthekera kokunva mawu) a zolengedwa zomwe zikutanthauza kuti palibe munthu amene angandiwelengere duruud kufikira tsiku la Qiyaamah kupatula kuti (Mngeloyu) amafikitsa duruuduyo kwa ine pamodzi ndi dzina lamunthuyo ndilabambo ake (adzanena kuti) uyu ndi uje mwana wa uje yemwe wakuwerengera duruud.’’
Read More »Salaat Ndi Salaam Zimufika Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasallam)
Sayyiduna Ibnu Abbaas (radhiyallahu anhuma) ulendo wina adati, “palibe munthu aliyense ochokera mu ummah wa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) amene amamufunira zabwino Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kupatula kuti Durood (imene anawerengayo) imafikitsidwa kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kudzera mwa angelo ndipo amauzidwa kuti munthu wakutiwakuti wakuwerengera Durood ndipo ujeni wakufunira zabwino pokuwerengera Durood.”
Read More »Adhaan – Chiyambi Chake 1
Mtumiki (sallallahua alaih wasallam) atapanga Hijrah (atasamukira) kupita ku Madina Munawwarah adamanga nzikiti. Atamanga nzikiti adakambirana ndi ophunzira ake nkhani yopezera njira imene angamawaitanire anthu kuti adzaswali. Lidali Khumbo la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti anthu adzisonkhana ndikuswalira pamodzi munzikiti. Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sankasangalatsidwa kuti masahabah adzaswali aliyense payekha …
Read More »Zikhulupiliro Zokhudza Angelo
10. Angelo amene amamufunsa munthu mafunso m’manda maina awo ndi Munkar ndi Nakiir.[1] ndipo mafunso omwe amafunsa ndi awa: a) Mbuye wako ndindani? b) Ungatiuze chani chokhuza Muhammad sallallah alaih wasallam? c) Chipembedzo chako ndi chiti?[2] 11. Mnsilamu aliyense ali ndi M’ngelo komanso shaitaan, M’ngelo amamulimbikitsa munthuyo kuchita zabwino ndipo …
Read More »Madalitso okamuzonda/kumuyendera Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)
Sayyiduna Ibnu Umar (radhiyallahu anhuma) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, "munthu amene angandiyendere Ine ndikadzamwalira ziri ngati wandiyendera Ndidakali ndi moyo."
Read More »Nthawi Zimene Miswak Ikufunika Kugwirtsidwa Ntchito
7. Pamene wina ali kumapeto kwa moyo wake (ali pafupi kumwalira).
Sayyidatuna Aisha (radhiyallahu anha) akufotokoza kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) atatsala pang’ono kumwalira nchimwene wanga amene ndi AbdulRahmaan (radhiyallahu anhu) adalowa mchipinda chomwe Mtumiki (sallallah alaih wasallam) adagona atanyamula miswaak yomwe ankagwiritsa ntchito kutsukira mkamwa.
Read More »Zikhulupiliro Zokhudza Angelo
6. Mikaa’eel (alaihis salaam) ndi amene amayang’anira zachakudya ndi nvula, angelo ena amagwira ntchito pansi pake ndipo amayang’anira mitambo nyanja mitsinje ndi mphepo, amauzidwa zoti achite ndi Allah ndipo kenaka amapeleka uthenga kwa angelo ena omwe ali pambuyo pake. 7. Israafeel (alaihis salaam) amalamuridwa ndi Allah kuti achotse mizimu ya …
Read More »Munthu Waumbombo
Sayyiduna Husain (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, munthu waumbombo kwambiri ndi amene amati akanva dzina langa samandifunira zabwino.
Read More »Nthawi Zimene Miswak Ikufunika Kugwirtsidwa Ntchito
4. Pamene mukupanga wuzu.
Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akuakufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih Wasalaam) adati, “chikhala kuti sichipsinjo pa ummah wanga ndikadawalamula (ndikadazipanga kukhala zokakamiza) kuti adzigwiritsa ntchito miswaak nthawi inailiyonse pamene akupanga wudhu (komano Sizili zokakamiza kutero koma ndisunnah yomwe yalimbikitsidwa pamene mukupanga wudhu).”
Read More »Zikhulupiliro Zokhudza Angelo
1. Angelo ndizolengedwa zomwe zilibe tchimo komanso adalengedwa kuchokera mukuwala, angelo samaoneka ndi maso athu, ndipo sii amuna kapena akazi. iwowa samadya kumwa kapena kugona monga amachitira munthu.[1] 2. Allah adawapatsa iwowa maudindo osiyanasiyana, amakwaniritsa lamulo lirilonse limene alamuridwa ndipo samanyozera malamulo a Allah.[2] 3. Sitimadziwa chiwelengero chenicheni cha Angelo …
Read More »