May 3, 2021
Uncategorized
27. Pangani itikafu (M´bindikiro) masiku khumi otsirizira a mwezi wa Ramadan ngati mungakwanitse kutero.
Olemekezeka Ibn Abbas (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adanena zokhudza kukhala mu itikafu kuti: ‘’Munthu amene akupanga itikafu (akubindikira munzikiti) amakhala kutali ndi machimo ndiponso nthawi yomweyo amalandila mphotho za ntchito zomwe akadatha kuzigwira pamene iye asali mu itikaafu.
Read More »
May 1, 2021
Masunna Ndi Aadaab (Miyambo)
15. Pangani masah m’makutu mwanu katatu pogwiritsa ntchito madzi atsopano, mukamapanga masah, gwiritsani ntchito chala chankomba phala mukamapaka mkati mwakhutu ndipo chala chachikulu kunja kwake (kuseli kwakhutu). kenako, tengani madzi ena ndikunyowetsa chala chaching’ono kapena chankomba phala ndikupanga m’mabowo a mkhutu ndipo pamapeto pake yendetsani manja anu m’makutu onse.[1] عن …
Read More »
April 29, 2021
Durood Ndi Salawaat
Olemekezeka Habbaan bin Munqiz (Rahimahullah) akusimba kuti Sahaba wina adamufunsa Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) nati "O inu Mtumiki Wa Allah Kodi ndingapereke gawo limodzi m’magawo atatu (one third) a nthawi yanga imene ndiri nayo pokuwerengerani Durood? Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adayankha nati, Inde ngati ungafune kutero, Ndiponso adafunsa nati kodi ndingaononge magawo awiri m’magawo atatu a nthawi yanga pokuwerengerani Durood? Rasulullah (sallallahu alayhi wasallam) adati inde ngati ungafune.Swahabayo adafunsanso nati kodi ndingaonongere nthawi yanga yonse pokuwerengerani durood? Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adayankha nati" Ngati ungachite zimenezi, Allah Ta’ala adzakukwaniritsira chirichonse chomwe ukuchifuna kaya za duniya (dziko lapansi) kapena zaku Aakhirat.
Read More »
April 26, 2021
Uncategorized
21.Kudzukira kudya Dakwi kuli ndi Madalitso ochuluka (Mabaraka).kotero, kwaniritsani Sunnah ya Dakwi musanayambe kusala.
Read More »
April 24, 2021
Masunna Ndi Aadaab (Miyambo)
12. Tengani madzi m’manja mwanu ndikutsuka dzanja lanu lamanja mpaka mwakasukusuku katatu. Kenako, tengani madzi m’manja mwanu ndikutsuka dzanja lanu lamanzere mpakana mwakasukusuku katatu. Ndi sunnah pamene mukuyamba kutsuka dzanja lanu kuyambira ku zala kumakwezeka mpaka mwakasukusuku, ngati wina wayambira akasukusuku kumatsika m’musi mpaka ku zala kutsuka kudzalandiridwa, komano zikusemphana ndi njira yasunnah yotsukira dzanja.
Read More »
April 22, 2021
Durood Ndi Salawaat
Sayyiduna Umar (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati "Kongoletsani mkumano wanu pondiwerengera Durood ine (kundifunila zabwino ine) chifukwa patsiku lachiweruzo durood idzakhala chobweretsa kuwala kwanu.
Read More »
April 19, 2021
Uncategorized
15. Pamene muli m’mwezi wa Ramadhan yesetsani kupanga ntchito zabwino. Hadith ina ikuti, ntchito ina iliyonse yabwino yomwe ungachite mwakufuna kwako (nafil ibaadah) m’mwezi wa Ramadhan (umalipidwa ndi Allah) ngati wachita chinthu cha faradh (chokakamizidwa kuchita) ndipo ngati wachita ntchito ya farad (yokakamizika kuchita) mumwezi wa Ramadan imaonjezeredwa malipiro ake …
Read More »
April 17, 2021
Masunna Ndi Aadaab (Miyambo)
9. Welengani duwa iyi nthawi ina iliyonse pamene mukupanga wudhu kapena mukamaliza wudhu. [1] اَللّٰهُمَّ اغْفِرْ لِيْ ذَنْبِيْ وَوَسِّعْ لِيْ فِيْ دَارِيْ وَبَارِكْ لِيْ فِيْ رِزْقِيْ Oh Allah, ndikhululukireni machimo anga, ndipatseni kutakasuka m’nyumba mwanga ndikundipatsa madalitso muchakudya changa. عن أبي موسى الأشعري رضي الله عنه قال أتيت رسول الله صلى …
Read More »
April 15, 2021
Durood Ndi Salawaat
Sayyiduna Samurah Suwaai (radhwiyallahu anhu), bambo a Jaabir radhwiyallahu anhu akufotokoza kuti, tsiku lina tidali pamodzi ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndipo kudabwera munthu wina namufunsa Mtumiki (sallallahu alaihi wasallam) kuti, oh Mtumiki wa Allah (sallallahu alaihi wasallam), ndi ntchito (ibadah) iti yomwe ndi yokondedwa kwambiri pamaso pa Allah?
Read More »
April 12, 2021
Uncategorized
8. Pamene Ramadhan ikubwera komanso tili mkati kati mwa Ramadhan yesetsani kumanena dua yotsatirayi: اَللّٰهُمَّ سَلِّمْنِيْ لِرَمَضَانَ وَسَلِّمْ رَمَضَانَ لِيْ وَسَلِّمْهُ لِيْ مُتَقَبَّلًا O Allaah nditetezeni ine pondifikitsa m’mwezi wa Ramadhan (ndili wa thanzi komanso nyonga ndicholinga choti ndipindule kwambiri m’mweziwu) komanso usamaleni mwezi wa Ramadhan kwa ine (poupangitsa kuti …
Read More »