26 Osaipitsira mumzikiti. mwachitsanzo kulavulira mumzikiti kapena kumina mumzikiti mpaka zoipazo maminawo kapena malovuwo mkugwera pansi munzikiti.[1] عن أبي ذر رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم عرضت علي أعمال أمتي حسنها وسيئها فوجدت في محاسن أعمالها الأذى يماط عن الطريق ووجدت في مساوئ أعمالها النخاعة …
Read More »Masunnah Ochita Mumzikiti
24. Sizili zoloredwa kumuchotsa munthu pamalo ake mumzikiti cholinga choti akhalepo wina.
Olemekezeka Ibnu Umar (radhwiyallah anhu) akunena kuti Mtumiki (salallah alayhi wasallama) adaletsa kuchotsedwa munthu wina pamalo ake ndikuti mumthu wina akhale pamalo ake. Choncho anthu akhoze malo oti akhale munthu amene (wabwera kumeneyo ngati zili zotheka kumupangira maloko).
Read More »Masunnah Ochita Mumzikiti
20. Osaimika swalah mumzikiti pa malo amene ungawatchingire anthu ena kudutsa mwaufulu. Mwachitsanzo kupemphera swalah pamalo polowera zimene zingapangitse ena kuti asadutse.
Olemekezeka Ibn Umar (radhiyallahu anhuma) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alayhi wasallama) adaletsa kupemphera swalah malo okwana asanu ndi awiri (ndipo amodzi mwamalowo) ndimalo odutsapo anthu.
Read More »Masunnah Ochita Mumzikiti
17. Osakangana ndiwina aliyense mumzikiti kumeneko ndikuonetsera kunyoza malo olemekezeka amzikiti.[1] 18. Ndipo ndizabwino kwambiri kuti musaupange mnzikiti kukhala njira yanu yodutsira popita tsidya lina.[2] عن ابن عمر رضي الله عنهما عن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال خصال لا تنبغي في المسجد لا يتخذ طريقا ولا يشهر فيه سلاح …
Read More »Masunnah Ochita Mumzikiti
14. Onesetsani kuti mwathimisa foni yanu pamene mukulowa mumzikiti ndicholinga choti musasokoneze nayo anthu amene ali otangwanika ndimapemphero ndi ma ibaada ena ndi ena.[1] 15. Osajambula mafoto kapena kupanga vidiyo pamene muli mumzikiti. Kujambula foto komanso kupanga vidiyo chinthu chamoyo ndi Haraam mchisilamu. ndipo kuchita zimenezi mumzikiti nditchimo lalikulu. عن …
Read More »Masunnah Ochita Mumzikiti
13. Osakweza mawu kapena kuphokosera mumzikiti komanso malo onse odzungulila mnzikiti.
Olemekezeka Saib bin Yazeed akusimba kuti; Nthawi ina yake ndinali kugona munzikiti ndipo munthu wina anandiponya timiyala ting´ononoting´ono (ndicholinga chondidzusa), ndidayang´ana ndiye ndidapeza kuti adali Umar (radiyallah anhu). Iye adati kwa inept; Pita undibweresere anthu awiri amenewa kwa ine (amene akutsokoserawa), Ndipo ndinawabweretsa kwa Umar (radiyallah anhu), ndipo anawafunsa nati, Inu ndiochokera kuti? Iwo adayankha nati ndife ochokera ku Taif. Olemekedzeka Umar (radiyallah anhu) adati Inuyo mukadakhala ngati anthu amumadinah muno ndikadakupasani chilango chokhwima kwambiri Mukukweza inuyo mawu mumzikiti wa Mtumiki (salallah alayhi wasallama).
Read More »Masunnah Ochita Mumzikiti
9. Pangani chitsimikizo kuti mukupanga itikafu ya sunnah (nafl itikaaf) panthawi imene mungakhalire mumzikitimo.
10. Pempherani maraka awiri a Tahiyyatul masjid (olemekedzera mzikiti) pamene mwangolowa mumzikiti kumene.
Read More »Masunnah Ochita Mumzikiti
7. Lowani mumzikiti ndimwendo wamanja.
Kwanenedwa kuti Olemekezeka Anas radhiyallahu anhu adati; ndipo ndi sunnah (njira yamtumiki sallallah alayhi wasallam) pamene ukulowa mumzikiti kulowa ndimwendo wamanja ndipo potuluka kutsogoza mwendo wamanzere.
Read More »Masunnah Ochita Mumzikiti
6. Werengani maduwa pamene mukupita kumzikiti. Ena mwa maduwawo ndi awa: Dua yoyamba Amene angawerenge duwa iyi pamene akunyamuka ulendo wakumzikiti amakhala ndichifundo cha Allah chapadera ndiponso angelo okwanira 70,000 amamuchitiranso maduwa.[1] اَللّٰهُمَّ إِنِّيْ أَسْأَلُكَ بِحَقِّ السَّائِلِيْنَ عَلَيْكَ وَأَسْأَلُكَ بِحَقِّ مَمْشَايَ هٰذَا فَإِنِّيْ لَمْ أَخْرُجْ أَشَرًا وَلَا بَطَرًا وَلَا رِيَاءً …
Read More »Masunnah Ochita Mumzikiti
6. Werengani maduwa pamene mukupita kumzikiti. Ena mwa maduwawo ndi awa:
Dua yoyamba
Amene angawerenge duwa iyi pamene akunyamuka ulendo wakumzikiti amakhala ndichifundo cha Allah chapadera ndiponso angelo okwanira 70,000 amamuchitiranso maduwa.
Read More »