Masunna Ndi Aadaab (Miyambo)

Kasambidwe Ka Sunnah-Gawo 3

9. Pangani wudhu onse.

Sayyidatuna Aaishah (radhiyallahu anha) akunena kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankati akamakasamba (kusamba kwa fardh) ankayamba ndikusamba m’manja asanalowetse manjawo m’madzi, kenaka ankatsuka malo obisika kenaka ankapanga wudhu ngati m’mene ankapangira(wudhu) akafuna kuswali.

Read More »

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo La chisanu Nchinayi

25. Ngati mbali iliyonse yachiwalo chomwe ndi fardh kusambitsa pamene mukupanga wudhu yasiidwa osasambitsa, wudhu udzakhala opelewera.

Sayyiduna Umar (radhwiyallahu anhu) akunena kuti munthu anapanga wudhu nasiya malo amodzi osasambitsa kuphanzi kwake mlingo wachikhadabu poyang’anitsitsa malo amenewo Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anamuuza iye kuti “pita ukamalizitse kupanga wudhu wako.”

 

Read More »

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo La Chisanu Nchiwiri

18. Mukamaliza wudhu, welengeni shahaadah ngati muli malo otakasuka, popanga shahaadah[1] yang’anani kumwamba, momwemonso werengani duwa iliyonse yomwe imabwera m’mahadith. Ena mwamaduwa a sunnah amene anenedwa m’mahadith oyenera kuwerengedwa pamapeto popanga wudhu ndi awa m’musimu: Duwa yoyamba: Amene angawerenge duwa imeneyi makomo asanu ndi atatu a ku Jannah amatseguka kuti …

Read More »

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo Lachisanu Nchimodzi

15. Pangani masah m’makutu mwanu katatu pogwiritsa ntchito madzi atsopano, mukamapanga masah, gwiritsani ntchito chala chankomba phala mukamapaka mkati mwakhutu ndipo chala chachikulu kunja kwake (kuseli kwakhutu). kenako, tengani madzi ena ndikunyowetsa chala chaching’ono kapena chankomba phala ndikupanga m’mabowo a mkhutu ndipo pamapeto pake yendetsani manja anu m’makutu onse.[1] عن …

Read More »

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo lachisanu

12. Tengani madzi m’manja mwanu ndikutsuka dzanja lanu lamanja mpaka mwakasukusuku katatu. Kenako, tengani madzi m’manja mwanu ndikutsuka dzanja lanu lamanzere mpakana mwakasukusuku katatu. Ndi sunnah pamene mukuyamba kutsuka dzanja lanu kuyambira ku zala kumakwezeka mpaka mwakasukusuku, ngati wina wayambira akasukusuku kumatsika m’musi mpaka ku zala kutsuka kudzalandiridwa, komano zikusemphana ndi njira yasunnah yotsukira dzanja.

Read More »

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo lachinayi

9. Welengani duwa iyi nthawi ina iliyonse pamene mukupanga wudhu kapena mukamaliza wudhu. [1] اَللّٰهُمَّ اغْفِرْ لِيْ ذَنْبِيْ وَوَسِّعْ لِيْ فِيْ دَارِيْ وَبَارِكْ لِيْ فِيْ رِزْقِيْ Oh Allah, ndikhululukireni machimo anga, ndipatseni kutakasuka m’nyumba mwanga ndikundipatsa madalitso muchakudya changa. عن أبي موسى الأشعري رضي الله عنه قال أتيت رسول الله صلى …

Read More »

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo lachitatu

6. Chukuchani mkamwa ndikuthira madzi mphuno nthawi imodzi katatu. Kachukuchidwe kamkamwa ndikuthira madzi mphuno kali motere, choyamba tengani madzi mdzanja lanu lamanja, kenako, pogwiritsa ntchito madzi ena, tsukani mkamwa kamodzi otsalawo gwiritsani ntchito kutsuka mphuno, mudzabwereza zimenezi kawiri kotsalako pogwiritsa ntchito madzi ena ulendo wina uliwonse.

Read More »