Aqaaid

Zikhulupiliro Zokhudza Mtumiki Wa Allah Muhammad (Sallallah alayhi wasallam)

1. Mtumiki Muhammad (salallah alayhi wasallam) ndi Mtumiki otsirizira mwa atumiki onse a Allah. Palibenso Mtumiki wina yemwe adzatumizidwe padziko lapansi kudzaongolera anthu ku dziko lirilonse. Ngati wina wake ali ndi chikhulupiliro kuti kudzabwera mtumiki wina pambuyo pa Mtumiki Muhammad (salallah alayhi wasallam) munthu ameneyo ndi Kafiri (simsilamu) ndipo wasemphana …

Read More »

Mmene Allah Taala Amazisamalilira Zolengedwa Zake

1. Allah Taala ndi wachisoni kwambiri kwa akapolo ake. Ndipo Iye Allah amakonda kwambiri akapolo, wodekha kwa akapolo ake komanso opilira kwambiri. Iye amakhululuka machimo ndiponso amalandila kulapa kwa akapolo ake.[1] 2. Allah Taala ndi mwini chilungamo chonse. Iye sapondereza akapolo ake ngakhale mpang´ono pomwe.[2] 3. Allah Taala anamupatsa munthu …

Read More »

Zikhulupiliro zokhudza Allah – 2

6. Palibe chilichonse chofanana ndi Allah Taala mayina ake ndi mbiri zake. Iye ndiokwanilira ulemelero wake ndi mbiri zake, palibe chinachirichonse chofanana ndi Allah Ta'ala mphamvu kapena maonekedwe. Iye Allah Ta'ala alibe maonekedwe kapena mtundu ofanana ndicholengedwa chirichonse.

Read More »

Zikhulupiliro zokhudza Allah

1. Allah Ta ‘ala yekha ndamene akuyenera kumpembedza.

2. China chilichonse chisadapezeke pano padziko, kunalibe chilichonse kupatula Allah yekha, kenaka Allah adalenga chilichonse. Kupatula Allah, palibe amene alindi mphanu zolenga chinachirichonse kapena kupeleka moyo ndi imfa.

Read More »

Kufunika kokhala ndi chikhulupiliro chenicheni (choyenera)

Chipembedzo chachisilamu pamodzi ndi nsanamira zake chagona pa chikhulupiliro chenicheni, ngati zikhulupiliro za munthu ndizolakwika, ngakhale kuti sizingamutulutse m’chisilamu, ngakhale atachita ntchito zabwino zachisilamu, sangalandire malipiro amene Allah adalonjeza, chifukwa choti zikhulupiliro zake ndi tsinde lenileni lachisilamu ndizolakwika.

Read More »