Pa nkhondo ya Khaibar, Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) atapereka mbendera ya Chisilamu kwa Ali (radhwiyallahu ‘anhu), Ali (radhwiyallahu ‘anhu) adatsogolera gulu lankhondo. Maswahaaba ku bwalo la Qamoos. Atayandikira bwalolo, msilikali wina wachiyuda, dzina lake Marhab, anatuluka kudzamenyana nawo. Marhab anali msilikali otchuka amene anali wodziwika ndi mphamvu zake zambiri ndi …
Read More »Mantha a Olemekezeka Ali (radhwiyallahu ‘anhu) kuliopa tsiku la Qiyamah
Kumail bin Ziyaad (rahimahullah) akuti: Nthawi ina ndinatsagana ndi Ali (radhwiyallahu ‘anhu) pamene ankatuluka mumzinda wa Kufah ndikupita ku Jabbaan (kumapeto kwa mzinda wa Kufah). Atafika ku Jabbaan, Ali (Radhwiyallahu ‘anhu) anatembenukira kumanda ndikufuula. “E inu anthu okhala m’manda! E, inu anthu amene matupi awo anavunda! E inu anthu osungulumwa! …
Read More »Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamuika Sayyiduna Ali (radhwiyallahu ‘anhu) kutsala ku Madina Munawwarah
Pa nthawi ya Nkhondo ya Tabuuk, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) pochoka ku Madinah Munawwarah, adamusankha Ali (radhiyallahu ‘anhu) kuti aziyang’anira ntchito za m’ Madina Munawwarah pakakhala kuti iye kulibe. Choncho, ndi malangizo a Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam), Ali (radhwiyallahu ‘anhu) sadatuluke ndi gulu lankhondo, koma adakhalabe ku Madina Munawwarah. Pambuyo …
Read More »Kulimba Mtima kwa olemekezeka Ali (radhiyallahu ‘anhu)
Pa nkhondo ya Uhud, Sayyiduna Ali (radhwiyallahu ‘anhu) adawonetsa kulimba mtima kwambiri polimbana ndi adaniwo. Choncho, iye yekha ndiye anali ndi udindo opha atsogoleri anayi a chiQuraishi, omwe mwa iwo anali Talhah bin Abi Talhah. Nkhondo itatha, adapereka lupanga lake kwa mkazi wake olemekezeka, Bibi Faatimah (radhwiyallahu ‘anha), kuti atsuke …
Read More »Chikondi cha olemekezeka Ali (radhwiyallahu ‘anhu) pa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam)
Nthawi ina yake Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) analibe chakudya choti adye kotero adavutika ndi njala. ‘Ali (radhwiyallaahu ‘anhu) atamva kuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) akumva njala, nthawi yomweyo mtima wake unadzazidwa ndi nkhawa ndi malingaliro. Chimenecho chinali chikondi chake pa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) kuti sadapume bwino pomwe adadziwa kuti …
Read More »Dua ya Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) kwa Ali (radhwiyallahu ‘anhu) potumiza ku Yemen
Ali (radhwiyallahu ‘anhu) akuti: Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adanditumiza monga bwanamkubwa wake ku Yemen. Ndisananyamuke ndidalankhula naye ndipo ndidati: “E, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Inu mukunditumiza kwa anthu akuluakulu kuposa ine. Kuonjezera apo, ine ndiine mwana, ndipo ndilibe kuzindikira kulikonse pa kaweruzidwe kamilandu. Atamva nkhawa zanga, Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) …
Read More »Kugula Malo Oonjezera Musjid-ul-Haraam
Nthawi ina Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adapita kwa munthu wina ku Makkah Mukarramah ndipo anati kwa iye, “O wakuti-ndi-wakuti! Kodi ungandigulitseko nyumba yako, kuti ndiwonjezereko nzikiti mozungulira Ka’bah, ndipo mu mphotho ya ntchito yabwinoyi, ndikukutsimikizira kuti udzakhala ndi nyumba yachifumu ku Jannah (kuwonjezera pa ndalama za nyumba yomwe utapatsidwe)?” Munthuyo …
Read More »Kukonzekera nkhondo ya Tabuuk
Abdur Rahmaan bun Khabbaab (radhwiyallah anhu) akufotokoza motere: Ndinalipo pamene Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ankawalimbikitsa ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) kuti akonzekeretse asilikali ndi kutenga nawo gawo pa ulendo wa Tabuuk. Nthawi imeneyo Uthmaan (radhwiya allahu ‘anhu) adayimilira nati: “Oh Mthenga wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Ine ndikupereka ngamila zana limodzi …
Read More »Kukhudzika pa Nkhani ya Kuyankha Mafunso pa Tsiku Lomaliza
Nthawi ina yake “Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adalowa m’khola lake la ziweto ndipo adapeza kapolo wake akudyetsera ngamira. Atachiona chakudyacho Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) sadasangalatsidwe ndi mmene kapoloyo adachikonzera kotero adapotokora khutu lake. Patangopita nthawi pang’ono, atalingalira zomwe wachita, ‘Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adada nkhawa ndikuopa kuti sangamutsegulire mlandu pa zimene wachita tsiku …
Read More »Makhalidwe khumi apadera a Uthmaan (radhwiyallahu anhu)
Hazrat Abu Thawr (rahimahullah) akuti tsiku lina adadza kwa Uthmaan (radhwiyallah”anhu) ndipo adamumva akunena izi panthawi yomwe adaukiridwa. Adati: “Pali ntchito zabwino zokwana khumi zomwe ndadziteteza kwa Allah Taala, ndipo pa ntchito iliyonse ndikuyembekeza kudzalandira malipiro pa tsiku lomaliza; 1) Ndinali munthu wachinayi kuvomereza Chisilamu. 2) Sindinanenepo bodza moyo wanga …
Read More »