Ngakhale Allah Ta’ala adamudalitsa Umar (radhwiyallahu ‘anhu) pokhala m’gulu la anthu khumi omwe adalonjezedwa kukalowa ku Jannah ali padziko lino lapansi, ndipo ngakhale adali khalifah wachiwiri wa Chisilamu, adali wodzichepetsa kwambiri ndikuwopa kuyankha mafunso pamaso pa Allah Ta’ala pa tsiku la Qiyaamah. Zikunenedwa kuti nthawi ina, Olemekezeka Umar (radhwiyallahu ‘anhu) …
Read More »Hazrat Ali (radhwiyallaahu ‘anhu) Akufuna Kukumana ndi Allah Ta’ala ndi zochita za Hazrat Umar (radhwiyallaahu ‘anhu)
Olemekezeka Abdullah bin Abbaas (radhwiyallaahu ‘anhuma) akunena kuti: Ndinalipo pa nthawi yomwe mtembo wa Umar (radhwiyallahu ‘anhu) unkaikidwa pa Jeneza ataphedwa. Anthu anayamba kuthamangira pamene padali thupi lake. Pamene ankayembekezera kuti mtembo wake utulutsidwe ndi kuikidwa m’manda, iwo ankawerenga durood kumfunira zabwino Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndikumamupemphera Umar (radhwiyallahu ‘anhu). …
Read More »Chisangalalo cha Hazrat Umar (Radhiyallahu ‘anhu)
Olemekezeka Umar (Radhwiyallaahu ‘anhu) adanenapo nthawi ina kwa olemekezeka Abbaas (Radhwiyallahu ‘anhu) (amalume a Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)) kuti: “Ndidakondwera ndi Chisilamu chanu kuposa Chisilamu cha abambo anga chifukwa Chisilamu chanu chidabweretsa chisangalaro chochuluka kwa Rasulullah swallallahu ‘alaihi wasallam) kuposa Chisilamu cha bambo anga. (Sharhu Ma’aanil Aathaar 3/321)
Read More »Hazrat Abu Bakr (Radhiyallahu ‘Anhu) Kuteteza Mtumiki (swallallahu alaih wasallam)
Nthawi ina, pamene Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) akuswali ku Ka’bah Shareef, Uqbah bin Abi Mu’ait, mmodzi mwa atsogoleri oipa a maquraish, adadza kwa iye ndi cholinga choipa chofuna kumuvulaza. Atafika kwa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam), Uqbah adavula nsalu yake, naiika m’khosi mwake nayamba kum’nyonga nayo mopanda chifundo. Hazrat Abu …
Read More »Hazrat Abu Bakr – manthu cha Ubwino ndi Chifundo
Tsiku lina Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adafunsa kwa ma Swahaabah (radhwiyallahu “anhum) kuti: “Ndani mwa inu amene akusala kudya lero?” Hazrat Abu Bakr (radhiyallahu anhu) adayankha: “Lero ndasala. Kenako Nabiy (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adafunsa. “Ndani mwa inu amene wayendera munthu wodwala lero?” Harrat Abu Bakr (radhiyallahu ‘anhu) adayankha: “Lero ndayendera …
Read More »Munthu Woyamba wa Ummah uwu kukalowa ku Jannah
M’ Hadith ya yodaliysika, Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adalongosora kuti Ummah wake udzalowa ku Jannah pamaso pa ma Ummah ena onse, ndipo kuchokera mu Ummah wake wonse, Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) adzakhala munthu woyamba kulowa ku Jannah pambuyo pake. Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Hazrat Jibreel (‘alaihis salaam) adaonekera …
Read More »Hazrat Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) akhala Wokonzeka kupereka nsembe ya china Chilichonse
Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa sallam) Pankhondo ya Badr, mwana wa Abu Bakr Siddeeq (radhwiyallahu anhu) Hazrat Abdur Rahmaan (Radhwiyallahu ‘anhu), anamenya nawo mbali ya okanira poti iye adali asadakhulupirirebe Chisilamu. Pambuyo pake, atalowa Chisilamu, ali chikhalire pansi ndi bambo ake, Hazrat Abu Bakr Siddeeq (Radhwiyallahu “anhu), adati: “E, inu abambo …
Read More »Chikondi cha Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) Kugwirizana ndi Chikondi cha Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam)
Bambo ake a Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) atalowa Chisilamu. Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) adalankhula kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) kuti: “Ndikulumbirira amene anakuikani m’choonadi! Ngakhale ndiri mchisangalaro kuti bambo anga alowa chisilamu, ndikadakhala osangalala kwambiri zikanakhala kuti omwe alowa chisilamu ndi amalume anu Abu …
Read More »Olemekezeka Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) amutumikira Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)
Hazrat Abu Bakr Siddeeq (Radhwiyallaahu ‘anhu) akusimba motere za ulendo wa Hijrah ndi Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam): Tinayenda mofulumira usiku wonse ndi gawo lina la tsiku lotsatira mpaka kutentha kwamasana kunakula kwambiri. Kenako ndinapeza kuti mseu mulibe munthu aliyense woyendamo. Ndinayang’ana kutsogolo kuti ndione ngati ndingapeze mthunzi uliwonse kuti tibisalemo. …
Read More »Ulemu wa Hazrat Abu Bakr (Radhiyallahu ‘anhu) kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ndi chikondi cha Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) pa Iye
Pa nthawi ya Fat-he-Makkah Mukarramah (Kugonjetsa Makka Mukarramah), Hazrat Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) adabweretsa bambo ake, Abu Quhaafah, kwa Rasulullah kuti akalowe Chisilamu. Pa nthawiyo Abu Quhaafah adali ndi zaka zoposa 90 zakubadwa ndipo adali atasiya kuona. Atadza kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam), Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamuuza Hazrat Abu …
Read More »