Sahaabah

Munthu Wabwino Kwambiri pa Ummah uwu

Hazrat Abu Dardaa radhiyallah anhu wanena kuti: “Nthaŵi ina yake, Mtumiki (Swallallaahu alaih wasallam). adandiona ndikuyenda kutsogolo kwa Hazrat Abu Bakr (Radhiyallahu ‘anhu) “Pamene Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adaona izi, adandiuza kuti: “Usayende kutsogolo kwa amene ali wabwino kuposa iwe. Pambuyo pake Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi …

Read More »

Hazrat Abu Bakr Siddeeq (Radhwiyallahu ‘anhu) ali m’phanga la Thaur

Ali kuphangako paulendo wa Hijrah, zikunenedwa kuti Hazrat Abu Bakr Siddeeq (radhwiyallahu anhu) adali ndi nkhawa kuti palibe cholengedwa chomwe chingatuluke mu dzenje lililonse la mphangamo ndi kuvulaza Hazrat Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam). Choncho, anayamba kutseka mabowo onse a m’phangamo ndi zidutswa za malaya ake apansi. Komabe, padali mabowo awiri …

Read More »

Olemekezeka Abu Bakr (Radhwiyallahu anhu) Kupereka Chuma Chake Kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)

Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallah alayhi wasallam) adati: “Palibe chuma cha munthu chomwe chidandipindulira monga chuma cha Abu Bakr (radhiyallahu anhu), atamva izi olemekezeka Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) adayamba kulira nati: “Chuma changa ndi zonse ndi zanu. Pali nkhani ya olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) m’buku …

Read More »

Chikondi cha Hazrat Anas bin Nadhr pa Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) Kuphedwa ku Uhud

Pamene Asilamu adagonjetsedwa ku Uhud, mphekesera zidayamba kufalikira kuti Sayyiduna Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) waphedwa. Nkhaniyi idawapangitsa ambiri mwa ma Swahaabah kutaya mtima ndi kutaya chiyembekezo. Sayyiduna Anas bun Nadhr adawona Hazrat Umar ndi Hazrat Talhah pamodzi ndi gulu la ma Sahaabah ali mu chisoni chachikulu ndi kutaya mtima. Iye …

Read More »

Answaari wina agwetsa nyumba pansi

Tsiku liina Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) ankadutsa mumsewu wa Madinah Munawwarah pamene adawona nyumba yomwe inali ndi dome. Adafunsa kwa Swahaabah. “Ichi ndi chiyani?” Anamuuza kuti inali nyumba yatsopano yomangidwa ndi mmodzi wa ma Ansaar. Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) anakhala chete. Tsiku lina, Answaari amene adamanga nyumbayo adadza …

Read More »

Hazrat Bilaal (Radhiya Allaahu ‘anhu) pa imfa yake

Pamene Hazrat Bilaal (Radhiya Allaahu ‘anhu) adatsala pang’ono kumwalira, mkazi wake adayamba kunena kuti: “Ha! Ndi zomvetsa chisoni bwanji! Mukuchoka m’dziko lino!” Hazrat Bilaal (Radhiya Allahu anhu) anayankha kuti: “Zili zokondweretsa ndi zosangalatsa kuti mawa tikukakumana ndi abwenzi athu, tikakumana ndi Muhammad (Swalla Allaahu ‘alayhi wa sallam) ndi maswahaba ake.”

Read More »

Nsembe ya maswahabah radhwiyallahu anhum pa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam)

Nyumba ya Bibi Faatimah (radhiyallahu anha) idali potalikirako ndi nyumba ya Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Tsiku lina Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamuuza kuti “khumbo langa ndiloti udzikhala nane pafupi” Bibi Faatimah (radhiyallahu anha) adayankha nati, Nyumba ya Haarithah ili pafupi ndi yanu, ngati mungamupemphe kuti tisinthanitse ndi yanga adzavomera mwansangala. …

Read More »

Palibe malo mu Chisilamu kwa amene a kunyoza ma Swahaabah (Radhiyallahu anhum)

Tsiku linalake Munthu wina anafika kwa Zainul Aabidiin, Aliy bin Husain rahimahullah ndipo adafunsa: Oh chidzukulu cha Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) maganizo anu ndi otani pa nkhani ya Uthmaan (radhwiyallahu anhu)? Atazindikira za nkwiyo wa munthuyu pa Uthmaan (radhwiyallahu anhu, Olemekeza Zainul Aabidiin (rahimahullah)adamulongosolera munthuyo kuti: Oh m’bale wanga okondeka! …

Read More »

Mphavu za Aliyy (radhiyallahu anhu) pa nkhondo ya Uhud

Pa nkhondo ya Uhud ma swahabah (radhwiyallahu anhum) adagonjetsedwa kwambiri ndi adani ndipo ambiri adaphedwa kumene, Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) Adazunguliridwa ndi adani ndikuvulazidwa kwambiri, nthawi imeneyi mphekesera idayamba kumveka kuti Mtumiki waphedwa, maswahabah atamva mphekesera imeneyi adasweka mitima ndikutaya chiyembekezo. Hazrat Ali (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti: tidazunguliridwa ndi adani …

Read More »

Olemekezeka Talhah (radhwiyallahu anhu) pa nkhondo ya Uhud

Olemekezeka Zubair bin Awwaam (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti pa nkhondo ya Uhud Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adaphatikiza zovala zozitetezera pa nkhondo. Mkatikati mwa nkhondo Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adafuna kukwera miyala ikulu ikulu koma ankakanika chifukwa chakulemera kwa zovala za pa nkhondo.Choncho adamupempha Olemekezeka Talha (radhwiyallahu anhu) kuti akhale pansi …

Read More »