Yearly Archives: 2024

Surah Zokhala ndi nthawi zake zowerenga komanso nthawi zake zosiyanasiyana zomwe zikuyenera kuwerenga 4

9. Werenganinso ayah zitatu zomaliza za Surah Baqarah musanagone. Kwanenedwa kuti Ali (Radhwiyallahu anhu) adati: “Sindikuganiza kuti aliyense wanzeru angagone popanda kuwerenga ma aya (atatu) omaliza a Surah Baqarah, chifukwa ndithu iwowo ndi chuma chochokera pansi pa Arsh. 10. Werengani Surah Faatihah ndi Surah Ikhlaas musanagone. Anas (Radhwiyallahu anhu) akusimba …

Read More »

Surah Zokhala ndi nthawi zake zowerenga komanso nthawi zake zosiyanasiyana zomwe zikuyenera kuwerenga 3

6. werengani Surah Sajdah musanagone. Olemekezeka Jaabir (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) sankagona mpaka atawerenga Surah Sajdah ndi Surah Mulk.[1] Khaalid bin Ma’daan rahimahullah, Taabi’ee, adatchula izi: “Ndithu Surah Sajdah idzakangana m’manda poteteza amene ankaiwerenga. Idzati, ‘O, Allah! Ngati ndili ochokera ku chitaab Chanu, muvomereni chiwombolo changa …

Read More »

Kulandira dzina loti ‘Mthandizi Wapadera’ wa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)

Pankhondo ya Ahzaab, yomwe imadziwikanso kuti Nkhondo ya Khandaq (Nkhondo ya Ngalande), Asilamu adalandira uthenga kuti Banu Quraizah adaswa lonjezo lawo loti adzakhulupirika kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndipo adajoina adani. Kuti atsimikize zomwe zamvekazi, Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawafunsa ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) kuti: “Ndani andibweretsere nkhani za anthu …

Read More »

Surah Zokhala ndi nthawi zake zowerenga komanso nthawi zake zosiyanasiyana zomwe zikuyenera kuwerenga 2

4. Werengani Surah Yaasiin m’mawa ndi madzulo aliwonse. Ibnu Abbaas (Radhwiyallahu anhu) adati: “Amene angawerenge Surah Yaasiin m’bandakucha, ntchito yake ya tsiku lonse idzafewetsedwa, ndipo amene angaiwerenge madzulo, ntchito yake mpaka m’mawa idzafewetsedwa.”[1] Olemekezeka Jundub (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anati: “Amene angawerenge Surah Yaasiin usiku ndi …

Read More »

Mabala owapeza munjira ya Allah Ta’ala

Hafs bin Khaalid (rahimahullah) akusimba kuti bambo wina wachikulire yemwe adafika kuchokera ku Mewsil adamuuza kuti ndidatsagana ndi Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) pa umodzi mwa maulendo ake. Pa nthawi ya ulendo. Pamene tinali malo otseguka, ouma, Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) ankafunika kusamba. Anatero kwa ine. “Ndibiseni (ndi nsalu kuti ndisambe).” Ndinamubisa motero, …

Read More »

Swalaah Ndi Kiyi Yaku Jannah

Chisilam ndi njira yokhayo imene imamutsogolera munthu ku chikondi cha Allah Ta’ala komanso chimamutsogolera Jannah. kudzera mukutsatira machitidwe a chisilamu, Munthu adzapeza chisangalaro cha Allah Ta’ala komanso adzapedza chipambano chosatha. Muntchito zokakamizidwa zonse mchisilamu, swalah ndi imene ili pamwamba kwambiri pachikakamizo, Mtumiki wa Allah (Swallallah alayhi wasallam) adati; “Swalah ndi …

Read More »

Surah Zokhala ndi nthawi zake zowerenga komanso nthawi zake zosiyanasiyana zomwe zikuyenera kuwerenga

Pali Surah zina zomwe zalamuridwa kuti ziziwerengedwa nthawi yodziwika usiku ndi usana kapena masiku ena a sabata. Ndi mustahab kwa munthu kuwerenga ma surah amenewa mu nthawi yake yoikidwa. 1. Werengani Surah Kaafiroon musanagone. Olemekezeka Jabalah bun Haarithah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallah alaihi wasallam) adati: “Ukamakagona, werenga Surah …

Read More »

Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 10

23. Ngati mudaloweza pamtima gawo lina lake la Qur’an Majiid, onetsetsani kuti mukulibwereza nthawi zonse kuti musaiwale. Hadith yachenjeza za kunyalanyaza kuwerenga Quraan ndi kuiwala zomwe waloweza pamtima.[1] Olemekezeka Abu Musah Ash’ari (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah Adati: “Isamareni Qur’an Majiid. Ndikulumbirira Amene m’manja Mwake muli moyo wanga, (Qur’an Majiid) …

Read More »

Olemekezeka Zubair (Radhwiya Allahu ‘anhu) Asolola Lupanga Lake Kuti Amutetezere Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam)

Olemekezeka Urwah bun Zubair (rahimahullah) akufotokoza motere Nthawi ina yake, Shaitaan anafalitsa mphekesera yabodza yoti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) wagwidwa ndi ma Kuffaar gawo la kumtunda kwa Makka Mukarramah. Atamva mphekesera imeneyi, Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu), yemwe panthawiyo anali ndi zaka khumi ndi ziwiri zokha, nthawi yomweyo adanyamuka, nadutsa mchigulugulu …

Read More »