4. Nthawi yonyamuka, werengani masnuun dua ya paulendo.
بِسْمِ اللهِ اَلْحَمْدُ لِلّٰهِ سُبْحَانَ الَّذِيْ سَخَّرَ لَنَا هٰذَا وَمَا كُنَّا لَهُ مُقْرِنِيْنَ وَإِنَّا إِلٰى رَبِّنَا لَمُنْقَلِبُوْنَ اَلْحَمْدُ لِلّٰهِ اَلْحَمْدُ لِلّٰهِ اَلْحَمْدُ لِلّٰهِ اَللهُ أَكْبَرْ اَللهُ أَكْبَرْ اَللهُ أَكْبَرْ لَا إِلٰهَ إِلَّا اللهُ سُبْحَانَكَ اللّٰهُمَّ إِنِّيْ ظَلَمْتُ نَفْسِيْ فَاغْفِرْ لِيْ فَإِنَّهُ لَا يَغْفِرُ الذُّنُوْبَ إِلَّا أَنْتَ
M’dzina la Allah Talaa Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah Talaa Ulemerero ukhale wa Allah Talaa yemwe Watigonjetsera chokwerachi (kapena kuika chokwerachi m’manja mwathu) ngakhale kuti sitidathe kuchigonjetsa (popanda thandizo Lake). Ndithu, kwa Mbuye wathu ndiko kobwerera. Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah Talaa. Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah Talaa Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah Talaa. Allah Talaa ndiye wamkulu. Allah Talaa ndiye wamkulu. Allah Talaa ndiye wamkulu. Palibe wina opembedzedwa mwachoonadi koma Allah Talaa.(Allah Talaa) Ndinu oyera kwambiri, Oh Allah Talaa ndithudi ndadzipondereza ndekha choncho ndikhululukireni, chifukwa palibe amene amakhululuka machimo kupatula Inu.
5. Ndikwabwino kuyamba ulendo wanu Lachinayi, ngati ndizotheka kuti muyende ulendo wanu Lachinayi. Kuyamba ulendo tsiku lina lililonse ndikololedwanso.
Olemekezeka Kaab bun Maalik radhwiyallahu anhu adati: “chidali chizolowezi cha Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam akafuna kuyenda ulendo, nthawi zambiri amanyamuka Lachinayi.
Olemekezeka Ka’b bun Maalik radhwiyallahu anhu adati: “Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam adanyamuka Lachinayi kunkhondo ya Tabuk, ndipo ankakonda kunyamuka Lachinayi.”
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu