Kupeza Mwayi Opangiridwa Dua Ndi Angelo Okwana Zikwi Makumi Asanu Ndi Awiri (70,000) Olemekezeka Ali (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene amayendera odwala m’bandakucha, angero zikwi makumi asanu ndi awiri (70,000) amamupemphera chifundo kwa Allah mpaka madzulo; Amene angamuyendere odwala madzulo angelo okwana 70,000 amamupemphera chifundo …
Read More »Mlamu wa Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam)
Olemekezeka Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu) adakwatira akazi okwana anayi. Aliyense mwa akazi ake anayi anali pachibale ndi m’modzi mwa akazi olemekezeka a Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi waaalihi wasallam). Ndichifukwa chake Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adamuuza kuti: “(Ndiwe) mlamu wanga padziko lapansi ndi tsiku lotsiriza (kutanthauza kuti udzakhalanso mlamu wanga …
Read More »Kuyendera Odwala
Chipembedzo cha Chisilamu chimalimbikitsa ndi kulamula kuti munthu akwaniritse udindo umene ali nawo kwa Allah ndi udindo umene ali nawo kwa akapolo a Allah. Pankhani ya udindo ndi maufulu omwe munthu ali nawo pa akapolo a Allah, izi zikhoza kugawidwa m’mitundu iwiri ya maufulu. Mtundu oyamba ndi ufulu umene uli …
Read More »Kuwolowa kwambiri manja kwa Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu)
Mkazi wa Talhah (Radhwiyallahu ‘anha), Su’da bint ‘Awf al-Muriyyah anakambapo izi zokhudza mwamuna wake Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu): “Tsiku lina Talha analowa m’nyumba ali okhumudwa. Chavuta ndi chiyani? Kodi ndalakwitsa penapake mchifukwa ndikuwona kuti mukuonetsa kukhumudwa? Chonde ndiuzeni kuti ndithe kuchotsa kukhumudwa kwanu. Iye adayankha, “Ayi, siunandilakwire chilichonse, ndipo ndithudi, ndiwe …
Read More »Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 8
20. Musatemberere ana anu pamene mukupempha pa Swalah kapena nthawi ina iliyonse. Ndizotheka kuti temberero lanu litha kukumana ndi nthawi yomwe ma dua amayankhidwa. Olemekezeka Jaabir (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Musadzitemberere nokha, ana anu, akapolo anu, kapena chuma chanu.Temberero lanu likhoza kukumana ndi nthawi (yoyankhidwa) …
Read More »Kulandira dzina la Al-Fayyadh kuchokera kwa Mtumiki swallallahu alaihi wasallam
Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adampatsa olemekezeka Talhah (radhwiyallahu ‘anhu) dzina loti Al-Fayyaadh (munthu owolowa manja kwambiri) kangapo. Pansipa pali nkhani imodzi yotere: Pankhondo ya Zi Qarad, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adadutsa pachitsime cha Baisaan. Madzi a m’chitsimechi ankadziwika kuti ndi anchere. Rasulullah (Swalla Allaahu …
Read More »Zizindikiro za Qiyaamah 4
Zizindikiro Khumi Zikuluzikulu Za Qiyaamah Monga zilili kuti pali zisonyezo zambiri zing’onozing’ono za Qiyaamah zomwe zalembedwa Mmahaadith, momwemonso pali zisonyezo zikuluzikulu zambiri zomwe zatchulidwanso Mmahaadith. Zizindikiro zikuluzikulu ndi zinthu zofunikira kwambiri zomwe zidzachitike pa dziko lapansi pano Qiyaamah isanafike ndipo zidzalengeza kuyandikira kwa Qiyaamah. Ma Muhadditheen aika kubwera kwa Imam …
Read More »Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 7
18. Popempha mpempheni Mulungu kuti akudalitseni ndi aafiyah (ie kuti akudalitseni momasuka m’magawo onse a moyo wanu). Abbaas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti: “Nthawi ina ndinamufunsa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam): “E, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) wa Allah, ndiphunzitse duwa (yaphindu) imene ndiyenera kupempha kwa Allah. Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anayankha, “Pemphani …
Read More »Mzake wa Nabi Musah ‘Alaihis Salaam ku Jannah
M’chisilamu ntchito iliyonse yabwino ili ndi kuthekera kolumikizitsa munthu ndi Allah ndikumupezetsa sawabu ku umoyo omwe uli nkudza, komabe pali ntchito zina zimene ndi zapederadera pamanso pa Allah ndipo zimatha kukhala njira yopezera ubwino wa Dini yonse ndi ubwino wa dunya pamodzi. Zina mwa ntchito zimenezo ndi kuonetsa kukoma mtima …
Read More »Olemekezeka Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu) Kukwaniritsa Lonjezo Lake
Olemekezeka Talhah (Radhwiyallaahu ‘anhu) akuti: Ma Swahaabah (Radhwiya Allahu ‘anhum) adauza munthu wina okhala kumudzi kuti: “Pita ukafunse kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) kuti Allah Ta’ala akunena za ndani (m’ndime yotsatira ya Quraan Majeed)” (ma Sahaabah) ndi amene adakwaniritsa lonjezo lawo (ndi Allah Ta’ala lokhala okhazikika pankhondo okonzeka kupereka …
Read More »