Pankhondo ya Badr, bambo a Abu Ubaidah Radhwiyallahu anhu adapitiriza kumulondora kufuna kuti amuphe. Komabe, iye anapitirizabe kuwapewa bambo akewo kuti asakumane nawo n’kuwapha. Komabe, iwowa atayesetsa ndikukumanizana naye maso ndi maso ndipo panalibe njira ina yopulumutsira moyo wake koma kuwapha, iye anapita patsogolo ndi kuwapha. Apa ndipamene Allah Taala …
Read More »Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) aluza mano ake pa nkhondo ya Uhud
Pankhondo ya Uhud, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamenyedwa koopsa ndi adani ndipo mano awiri a chisoti chake chachitsulo chovala pankhondo adalowa mmatsaya ake odalitsika. Abu Bakr Siddiiq (Radhwiyallahu ‘anhu) ndi Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) nthawi yomweyo anathamanga kukamuthandiza Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam). Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) anayamba kuzula …
Read More »Kodi Amaanah Imatanthauza Chiyani?
Amaanah imatanthauza kuti munthu akhale olingalira za tsiku lachiweruzo pamene adzaime pamaso pa Allah pankhani ya maudindo amene munthu ali nawo kwa Allah ndi akapolo a Allah. Limeneri ndi khalidwe labwino kwambiri kotero kuti ndi khomo lopezera zabwino zosawerengeka za uzimu ndi thupi zochoka kwa Allah. Ubwino wa amaanah umapanga …
Read More »Nthawi Zomwe Ma Dua Amayankhidwa
Nthawi ya Azaan ndi Pamene Magulu Awiri Akumana Pankhondo Olemekezeka Sahl bin Sa’d (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallah alaihi wasallam) adati: “Pali nthawi ziwiri zomwe madua sangakanidwe kapena nthawi zambiri sangapande osayankhidwa; pa nthawi ya Azaan ndi pamene magulu awiri ankhondo akumana pankhondo.”[1] Pakati pa Azaan ndi Iqaamah Olemekezeka …
Read More »Khumbo la Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) kudalitsidwa ndi Chipinda Chodzaza ndi Anthu monga Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)
Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) nthawi ina anakhala pansi ndi gulu la maswahabah pamene iye analankhula nawo ndipo kenako anafunsa funso lonena kuti, “Tandiuzani chimene anthu inu mukulakalaka” Munthu wina adati: “Chokhumba chomwe ndili nacho ndikuti chipinda chonsechi chitadzadza ndi ma dirham (ndalama zasiliva) ndikuti ndiwononge zonsezo panjira ya Allah Ta’ala.” Umar …
Read More »Anthu Omwe Ma Duwa Awo Amayankhidwa 3
Munthu Wachikulire Okhala ndi invi Olemekezeka Anas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Ndithu Allah amachita manyazi kukana duwa ya munthu (okalamba) watsitsi loyera ngati ali olungama Munthu Opanga Dua Pagulu Olemekezeka Habiib bun Maslamah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Palibe gulu la …
Read More »Kudalirika Kwenikweni Kwa Olemekezeka Abu Ubaidah bin Jarrah (Radhwiyallahu ‘anhu)
Anthu a ku Najraan atalowa Chisilamu, adadza kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) namupempha kuti awatumizire munthu odalirika (yemwe angakawaphunzitse Swalah). Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati kwa iwo: لأبعثن إليكم رجلا أمينا حق أمين Ndidzatumizirani munthu okhulupirira ndi odalirika kwambiri. Pa nthawiyo, ma Swabsaabah (Radhwiyallahu anhum) omwe adalipo onse …
Read More »Anthu Omwe Ma Duwa Awo Amayankhidwa 2
Munthu Yemwe Akudwala Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu anahu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Mukakumana ndi odwala, mupempheni kuti akupangireni duwa chifukwa dua yake ili ngati dua ya angero (chifukwa cha kudwalako, machimo ake amakhululukidwa), choncho akufanana ndi angelo pokhala opanda machimo, ndipo potero pempho lake lidzalandiridwa mwachangu). Yemwe Amapanga …
Read More »Olemekezeka Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) Awapatsa ana ake aamuna maina pambuyo pa kuphedwa kwa ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum)
Olemekezeka Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) adanenapo kuti: “Ndithu, Talhah bin ‘Ubaidillah (Radhwiyallahu ‘anhu) amasunga mayina a Ambiyaa (‘alaihimus salaam) kwa ana ake, pomwe akudziwa kuti sipadzakhala Nabiy odzabwera pambuyo pa Mtumiki Muhammad (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam). Zubair (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adati: “Ndimasungira ana anga maina a mashahidi (achi Swahaabah) kuti mwinanso …
Read More »Anthu Omwe Ma Duwa Awo Amayankhidwa 1
Makolo, Wapaulendo ndi Oponderezedwa Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Ma dua atatu ndi otero kuti pangavute bwanji adzalandiridwa; dua ya bambo (kapena mayi, pa mwana wawo), dua ya musaafir (munthu wapaulendo) komanso dua ya oponderezedwa.”[1] Munthu Osala kudya komanso Mtsogoleri Wachilungamo Olemekezeka Abu …
Read More »