Masunna Ndi Aadaab (Miyambo)

Masunnah Ochita Mumzikiti

7. Lowani mumzikiti ndimwendo wamanja.

Kwanenedwa kuti Olemekezeka Anas radhiyallahu anhu adati; ndipo ndi sunnah (njira yamtumiki sallallah alayhi wasallam) pamene ukulowa mumzikiti kulowa ndimwendo wamanja ndipo potuluka kutsogoza mwendo wamanzere.

Read More »

Masunnah Ochita Mumzikiti

6. Werengani maduwa pamene mukupita kumzikiti. Ena mwa maduwawo ndi awa: Dua yoyamba Amene angawerenge duwa iyi pamene akunyamuka ulendo wakumzikiti amakhala ndichifundo cha Allah chapadera ndiponso angelo okwanira 70,000 amamuchitiranso maduwa.[1] اَللّٰهُمَّ إِنِّيْ أَسْأَلُكَ بِحَقِّ السَّائِلِيْنَ عَلَيْكَ وَأَسْأَلُكَ بِحَقِّ مَمْشَايَ هٰذَا فَإِنِّيْ لَمْ أَخْرُجْ أَشَرًا وَلَا بَطَرًا وَلَا رِيَاءً …

Read More »

Masunnah Ochita Mumzikiti

4. Pitani kumzikiti modekha ndi mwa ulemu. musapite mukuthamanga.

Olemekezeka Abu Hurayrah (radhiyallah anhu) adati; ndinamumva Mtumiki wa Allah (sallallah alayhi wasallam) akunena kuti; Pamene iqqamah yachitidwa, musapite kukapemphera swala pamene mukuthamanga, Mmalo mwake, Mukuyenera kuyenda modekha ndi mwaulemu. Gawo laswalah limene mwalipeza ndi Imaam, pempherani. Ndipo gawo lomwe lakudutsani kwanirisani. (pamene imaam watsiriza swalah)

Read More »

Masunnah Ochita Mumzikiti

1. Valani moyenera pamene mukupita kumnzikiti

Allah ta’ala akuyankhula kuti: Oh Inu ana Aadam (alyhi salaam), zikongoleseni (valani zovala zozikongoletsera) pamene mukupemphera swalah munzikiti

Read More »

Ma ubwino omwe munthu yemwe amakaswalira kunzikiti amapeza

4. Kupitapita kumzikiti ndi njira yokhayo yomwe ingateteze Dini ya munthu.

Sayyiduna Mu’adh bin Jabal (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, ndithudi satana ndi nkhandwe ya munthu (yomwe imansaka munthu kuti idye) monga m'mene nkhandwe ya ziweto imachitira yomwe imapezelera mbuzi yomwe ili yokhayokha, Pewani kukhala panokhanokha (kapena kutsata maganizo a okha) ndipo gwiritsitsani gulu la Ahlus-sunnah wal jamaa'ah ndikukhala limodzi ndi ummah komanso kulumikizana ndi mzikiti".

Read More »

Ma ubwino omwe munthu yemwe amakaswalira kunzikiti amapeza

1. Kupangira wudhu kunyumba komanso Kuyenda kupita kunzikiti ndi njira yokhululukidwa machimo ndikukwezedwa ulemelero.

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: Munthu amene angapange wudhu kunyumba ndi Kuyenda wapansi kupita kunzikiti kuti akakwaniritse lamulo la Allah phanzi lirilonse lomwe angaponye amakhulukidwa machimo, ndipo phanzi lina lomwe angaponye adzakwezedwa ulemelero wake.

 

Read More »

Maubwino a Mzikiti

1 Mizikiti imatengedwa kuti ndimalo okondedwa kwambiri pamaso pa Allah. عن أبي هريرة رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال أحب البلاد إلى الله مساجدها وأبغض البلاد إلى الله أسواقها (صحيح مسلم، الرقم: 671) Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (Sallallahu alaih wasallam) adati: …

Read More »

Nthawi Zimene Miswak Ikufunika Kugwirtsidwa Ntchito

7. Pamene wina ali kumapeto kwa moyo wake (ali pafupi kumwalira).

Sayyidatuna Aisha (radhiyallahu anha) akufotokoza kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) atatsala pang’ono kumwalira nchimwene wanga amene ndi AbdulRahmaan (radhiyallahu anhu) adalowa mchipinda chomwe Mtumiki (sallallah alaih wasallam) adagona atanyamula miswaak yomwe ankagwiritsa ntchito kutsukira mkamwa.

Read More »

Nthawi Zimene Miswak Ikufunika Kugwirtsidwa Ntchito

4. Pamene mukupanga wuzu.

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akuakufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih Wasalaam) adati, “chikhala kuti sichipsinjo pa ummah wanga ndikadawalamula (ndikadazipanga kukhala zokakamiza) kuti adzigwiritsa ntchito miswaak nthawi inailiyonse pamene akupanga wudhu (komano Sizili zokakamiza kutero koma ndisunnah yomwe yalimbikitsidwa pamene mukupanga wudhu).”

Read More »