Masunna Ndi Aadaab (Miyambo)

Ubwino ogwiritsa ntchito miswak

1. Kugwiritsa ntchito miswak kumaonjezera sawaabu za swalah ka 70.

Sayyiduna Aaishah radhiyallahu anha akunena kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, swalah imene yapempheledwa utagwiritsa ntchito miswak (popanga wudhu) ilindi sawaab zokwana 70 kuposa swalah yomwe yaswalidwa popanda kugwiritsa ntchito miswak.

Read More »

Kasambidwe Ka Sunnah-Gawo 4

14. Onetsetsani kuti madzi akufika pena paliponse pathupi lanu, nthawi ina iliyonse mukadzithira madzi dzinyureni ndicholinga chofuna kuonetsetsa kuti madziwo alowa pakhungu lonse, ngakhale kutangotsala malo ochepetsetsa kwambiri osathiridwa madzi, kusamba (kwa fardh) sikudzatheka, pamene mukusambitsa thupi, sambitsani kutsogolo kwake kenako kumbuyo.

Read More »

Kasambidwe Ka Sunnah-Gawo 3

9. Pangani wudhu onse.

Sayyidatuna Aaishah (radhiyallahu anha) akunena kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankati akamakasamba (kusamba kwa fardh) ankayamba ndikusamba m’manja asanalowetse manjawo m’madzi, kenaka ankatsuka malo obisika kenaka ankapanga wudhu ngati m’mene ankapangira(wudhu) akafuna kuswali.

Read More »

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo La chisanu Nchinayi

25. Ngati mbali iliyonse yachiwalo chomwe ndi fardh kusambitsa pamene mukupanga wudhu yasiidwa osasambitsa, wudhu udzakhala opelewera.

Sayyiduna Umar (radhwiyallahu anhu) akunena kuti munthu anapanga wudhu nasiya malo amodzi osasambitsa kuphanzi kwake mlingo wachikhadabu poyang’anitsitsa malo amenewo Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anamuuza iye kuti “pita ukamalizitse kupanga wudhu wako.”

 

Read More »

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo La Chisanu Nchiwiri

18. Mukamaliza wudhu, welengeni shahaadah ngati muli malo otakasuka, popanga shahaadah[1] yang’anani kumwamba, momwemonso werengani duwa iliyonse yomwe imabwera m’mahadith. Ena mwamaduwa a sunnah amene anenedwa m’mahadith oyenera kuwerengedwa pamapeto popanga wudhu ndi awa m’musimu: Duwa yoyamba: Amene angawerenge duwa imeneyi makomo asanu ndi atatu a ku Jannah amatseguka kuti …

Read More »