Yearly Archives: 2023

Mnyumba momwe Mukuwerengedwa Qur’an

M’ Hadith yolemekezeka, zatchulidwa kuti nyumba yomwe mumawerengedwa Qur’an Majiid imakhala ndi madalitso, kotero. Angelo amaunjikana mmenemo komanso chifundo cha Mulungu chimatsikira m’menemo. Zidanenedwa zokhudza nkhani ya olemekezeka Ubaadah Ibn Saamit (radhwiyallahu anhu) kuti “Nyumba yomwe imawerengedwa Qur’an ndenga lake limakutiridwa ndi Nuru imene angelo akumwamba amafunafuna chiongoko ndi kuwala …

Read More »

Kulimba Mtima kwa olemekezeka Ali (radhiyallahu ‘anhu)

Pa nkhondo ya Uhud, Sayyiduna Ali (radhwiyallahu ‘anhu) adawonetsa kulimba mtima kwambiri polimbana ndi adaniwo. Choncho, iye yekha ndiye anali ndi udindo opha atsogoleri anayi a chiQuraishi, omwe mwa iwo anali Talhah bin Abi Talhah. Nkhondo itatha, adapereka lupanga lake kwa mkazi wake olemekezeka, Bibi Faatimah (radhwiyallahu ‘anha), kuti atsuke …

Read More »

Kuwerenga Quraan Majeed

Allah wadalitsa Ummah wa Sayyiduna Muhammad swallallah alaihi wasallam ndi nyanja yopanda magombe. Nyanja iyi yadzadzidwa ndi ngale, ndi emarodi, ndi marubi, ndi zinthu zina za mtengo wapamwamba pa chuma. Kuchuluka kotenga zinthu mnyanja imeneyi ndiye kuchulukanso kwa phindu lomwe munthuyo angapeze. Nyanja imeneyi siidzatha koma idzapitiriza kumudalitsa munthu chimodzimodzi …

Read More »

Chikondi cha olemekezeka Ali (radhwiyallahu ‘anhu) pa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam)

Nthawi ina yake Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) analibe chakudya choti adye kotero adavutika ndi njala. ‘Ali (radhwiyallaahu ‘anhu) atamva kuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) akumva njala, nthawi yomweyo mtima wake unadzazidwa ndi nkhawa ndi malingaliro. Chimenecho chinali chikondi chake pa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) kuti sadapume bwino pomwe adadziwa kuti …

Read More »

Dua ya Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) kwa Ali (radhwiyallahu ‘anhu) potumiza ku Yemen

Ali (radhwiyallahu ‘anhu) akuti: Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adanditumiza monga bwanamkubwa wake ku Yemen. Ndisananyamuke ndidalankhula naye ndipo ndidati: “E, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Inu mukunditumiza kwa anthu akuluakulu kuposa ine. Kuonjezera apo, ine ndiine mwana, ndipo ndilibe kuzindikira kulikonse pa kaweruzidwe kamilandu. Atamva nkhawa zanga, Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) …

Read More »

Kugula Malo Oonjezera Musjid-ul-Haraam

Nthawi ina Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adapita kwa munthu wina ku Makkah Mukarramah ndipo anati kwa iye, “O wakuti-ndi-wakuti! Kodi ungandigulitseko nyumba yako, kuti ndiwonjezereko nzikiti mozungulira Ka’bah, ndipo mu mphotho ya ntchito yabwinoyi, ndikukutsimikizira kuti udzakhala ndi nyumba yachifumu ku Jannah (kuwonjezera pa ndalama za nyumba yomwe utapatsidwe)?” Munthuyo …

Read More »

Qunuut

3. Ndi sunnah kuswali Swalah ya Witr tsiku lililonse m’chaka chonse. Swalah ya Witri idzachitika mukatsiriza kuswali Fardh ndi Sunnah za Swalah ya Esha. M’chaka chonse, munthu akaswali Witr sangawerenge Qurnuot. Komabe zili sunnah kuwerenga Ounoot mu pa swala ya Witr mu theka lachiwiri la mwezi wa Ramadhaan (kuyambira pa …

Read More »

Kukonzekera nkhondo ya Tabuuk

Abdur Rahmaan bun Khabbaab (radhwiyallah anhu) akufotokoza motere: Ndinalipo pamene Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ankawalimbikitsa ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) kuti akonzekeretse asilikali ndi kutenga nawo gawo pa ulendo wa Tabuuk. Nthawi imeneyo Uthmaan (radhwiya allahu ‘anhu) adayimilira nati: “Oh Mthenga wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Ine ndikupereka ngamila zana limodzi …

Read More »

Qunuut

1. Ndi Sunnah kuwerenga Qunuut mu rakah yachiwiri ya Swalah ya Fajr. Qunuut idzawerengedwa mu rakah yachiwiri akaweramuka kuchokera pa Ruku. Adzayambe wawerenga tahmeed (ربنا لك الحمد) kenako adzayamba kuwerenga Qunut. 2. Powerenga Qur’an, munthu adzakweza manja ake mpaka pa chifuwa chake ndikuwerengaa dua monga momwe munthu amanyamulira manja ake …

Read More »

Kukhudzika pa Nkhani ya Kuyankha Mafunso pa Tsiku Lomaliza

Nthawi ina yake “Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adalowa m’khola lake la ziweto ndipo adapeza kapolo wake akudyetsera ngamira. Atachiona chakudyacho Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) sadasangalatsidwe ndi mmene kapoloyo adachikonzera  kotero adapotokora khutu lake. Patangopita nthawi pang’ono, atalingalira zomwe wachita, ‘Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adada nkhawa ndikuopa kuti sangamutsegulire mlandu pa zimene wachita tsiku …

Read More »