Pakati pa mphindi zomaliza pambuyo pa Hazrat Umar (radhiliyalahlah ‘Ahu) adaphedwa mwangozi, Anatumiza mwana wake, Hazrat Abdullah Bin Umar (radhwiyallahu ‘Anhuma), kunyumba kwa Hazrat Aaishah (radhiyallahu ‘ahha). Hazrat Umar (Radhiyallahu anhu adamulangiza iye kuti ukamuuze kuti Umar akupereka Salaam. Usakanene kuti Amiirul muuminiin popeza kuyambira lero sindidzaitanidwanso …
Read More »Yearly Archives: 2023
Kudzichepetsa kwa Sayyiduna Umar (Radhwiyallahu ‘anhu)
Olemekezeka Miswar bin Makhramah (radhwiyallahu ‘anhu) akusimba kuti pamene Umar (radhwiyallahu ‘anhu) anabayidwa, iye anayamba kumva chisoni ndi kukhala ndi nkhawa kwambiri kuudandaulira ummah. Ibnu Abbaas (radhwiyallahu ‘anhu) adamtonthoza nati: “Oh Ameer-ul-Mu’mineen! Palibe chifukwa chodandaulira. Mudakhala pamodzi ndi Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndipo mudakwaniritsa ma ufulu ake onse . Ubwenzi …
Read More »Mfundo Ya Imaam Shaafi’ee
Imaam Shaafi’e (rahimahullah) walemba mu chitabu chotchedwa Ikhtilaaful Hadith kuti: Sitikudziwa mwa akazi olemekezeka a Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) kusiya nyumba zawo ndikupita kunzikiti kukaswali Swalaah ya Jumuah kapena Swalah ina iliyonse, ngakhale kuti adali akazi olemekezeka a Sayyiduna Rasulullah chifukwa cha udindo wawo wapadera ndi ubale wawo ndi Mtumiki …
Read More »Ulemu wa Umar (radhwiyallahu ‘anhu) kwa Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu)
Hazrat Umar (radhiyallahu anhu) nthawi zonse ankavomereza udindo wapamwamba wa Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo sankadzitenga ngati iye ndi wofanana ndi Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu). Ulendo wina gulu la anthu linamutamanda Umar (radhwiyallahu ‘anhu) ponena kuti: “Ndikulumbirira kwa Allah! Sitinaonepo munthu wolungama, wonena zoona, ndi wokhwimitsa zinthu kwambiri kwa …
Read More »Zul Hijjah – Mwezi wa Haji ndi Qurbaani
Zul Hijjah ndi mwezi womaliza wa kalendala ya Chisilamu. Ngakhale mwezi wonse wa Zul Hijjah ndi wopatulika komanso wodalitsika, masiku khumi oyambirira a Zul Hijjah ali ndi kupatulika kwakukulu ndi ubwino. Ponena za masiku khumi oyambirira a Zul Hijjah, Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam wasallam) adati: “Masiku abwino kwambiri padziko lapansi …
Read More »Kukhudzika kwa Sayyiduna Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) pa Swalaah
M’mawa womwe Umar (radhwiya allaahu ‘anhu) adabayidwa, Olemekedzeka Miswar bin Makhramah (radhwiyallahu ‘anhu) adadza kudzamuona. Polowa mnyumba adapeza Umar (radhwiyallahu ‘anhu) atafunditsidwa ndi ndi nsalu ali chikomokere. Olemekezeka Miswar (radhwiyallahu ‘anhu) adafunsa anthu omwe adalipo pamenepo kuti, “Ali bwanji?” Iwo anayankha kuti: “Ali chikomokere monga mukuwoneramu.” Chifukwa panalibe nthawi yochuluka …
Read More »Tafseer Ya Surah Lahab
بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ تَبَّتْ يَدَا أَبِي لَهَبٍ وَتَبَّ ﴿١﴾ مَا أَغْنَىٰ عَنْهُ مَالُهُ وَمَا كَسَبَ ﴿٢﴾ سَيَصْلَىٰ نَارًا ذَاتَ لَهَبٍ ﴿٣﴾ وَامْرَأَتُهُ حَمَّالَةَ الْحَطَبِ ﴿٤﴾ فِي جِيدِهَا حَبْلٌ مِّن مَّسَدٍ ﴿٥﴾ Manja awiri a Abu Lahab awonongeke, ndipo awonongekeretu! chuma chake sichidampindulire ngakhalenso zomwe adapeza. Posachedwapa adzalowa m’moto wodzadza ndi malawi oyaka, komanso mkazi wake, woipa wonyamula nkhuni …
Read More »Hazrat Umar (radhwiyallahu ‘anhu) Kulemekeza Azwaaj-e-Mutahharaat (radhwiyallahu ‘anhunna)
Olemekezeka Aslam (rahimahullah), kapolo wa Sayyiduna Umar (radhwiyallahu anhu), akufotokoza kuti Umar (radhwiyallahu ‘anhu) anali ndi mbale zisanu ndi zinayi zomwe zidasungidwa kuti azitumizira mphatso kwa Azwaa-e-Mutwahharaat (akazi olemekezeka a Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) di amayi a Ummah). Olemekezeka Aslam (rahimahuliah) adanena kuti nthawi iliyonse kukafika chakudya chokoma, zipatso kapena …
Read More »Kapempheredwe ka Azimayi
Mazhab anayi Kuyambira nthawi ya Sayyiduna Rasulullah, ma Swahaabah, Taabi’een ndi zaka mazana zotsatira, akazi ankalamulidwa kuswali m’njira yosiyana ndi Swalaah ya amuna m’magawo ena za swalah. Madhabu onse anayi (omwe ndi Hanafi, Maliki, Shafi’i ndi Hambali) onse amagwirizana pa mfundo yakuti Swalaah ya akazi imasiyana ndi Swalaah ya amuna …
Read More »Kusamalitsa pa Chuma cha Anthu
Kusamalitsa komwe olemekezeka Umar (radhwiyallahu ‘anhu)adachita pa kagwiritsidwe ntchito ka chuma cha anthu kunalidi kosasimbika. Nthawi ina, musk (mtundu wa mafuta onunkhira) anabweretsedwa kuchokera ku Bahrain. Ngati chuma cha anthu onse, Umar (radhwiya allaahu ‘anhu) adati: “Ndikulumbirira kwa Allah! Ndikufuna nditapeza munthu wodziwa kuyeza zinthu kuti andipimire mafutawa kuti ndiwagawe …
Read More »