Abdullah bin Marzuuq rahmatullah alaihi anali kapolo oopa Allah komanso anali m’nthawi ya ma Muhaddithiin akuluakulu monga Sufyaan bun Uyainah ndi Fudhail bun Iyaadh Rahimahumallah. Poyamba, iye anali okonda moyo wa dziko lapansi ndipo sanali odzipereka ku Dini. Komabe, Allah adamudalitsa ndi tawfiiq (kuthekera) koti alape ndi kukonza moyo wake. …
Read More »Yearly Archives: 2024
Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 4
9. Pamene mukupanga dua, mtima wanu uyenera kukhala olunjika ndi kukhala ndi chidwi kwa Allah, Mtima wanu usakhale osalabadira komanso osaganizira pamene mukupanga dua. Musamamwaze maso kuwayang’ana anthu pamene mukupanga dua. Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Pemphani kwa Allah motsimikiza ndi mwachiyembekezo kuti …
Read More »Kudzipatula kwa Olemekezeka Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) ku Chuma Chadziko Lapansi
Umar (Radhiyallahu ‘anhu) atachoka ku Madina Munawwarah kupita ku Baitul Muqaddas kuti akagonjetse, adayima ku Syria kuti akakumane ndi ma Swahaabah omwe ankakhala kumeneko. MaSwahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) adadzakumana naye (Radhwiya Allahu ‘anhu) yemwe adali kukhala ku Syria ndi kulamulira Syria, adawafunsa: “Ali kuti m’bale wanga?” maSwahaabah (Radhwiyallahu ‘anhu) adafunsa: “Kodi …
Read More »Zizindikiro za Qiyaamah 1
Mma hadith odalitsika, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adalosera zizindikiro zomwe zidzachitike Qiyaamah isanafike. Adauchenjeza Ummah za mayesero ndi masautso osiyanasiyana omwe adzawapeze m’malo osiyanasiyana komanso pa nthawi zosiyanasiyana pa dziko lapansi. Adawasonyezanso njira ya chiongoko ndi chipulumutso ku fitnah. Uku ndiye kukongora kosayerekezeka ndi kupambana kwa Dini ya Chisilamu …
Read More »Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 3
6. Popanga dua, musagwiritse ntchito njira yokayikira. Mwachitsanzo, musanene kuti: “E Allah, ngati Mukufuna kundikwaniritsira zosowa zanga kwaniritsani; Olemekezeka Abu Hurayrah (Radhwiyallahu anhu) adasimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam adati; popanga dua m’modzi wa inu asanene kuti Ndichitireni chifundo ngati Mukufuna, ndikhululukireni ngati Mukufuna ndi ndipatseni mariziki ngati mujufuna.’ m’malo …
Read More »Chikhulupiliro cha Umar (radhwiyallahu ‘anhu) mwa Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)
Sayyiduna Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adafika kumalire a Shaam (Syria) atauzidwa za mliri omwe udawagwera anthu a ku Syria. Sayyiduna Umar (Radhiya Allaahu ‘anhu) adati: “Ngati imfa ingandifikire Abu ‘Ubaidah bin Jarraah (Radhiya Allaahu ‘anhu) akadali ndi moyo, ndiye kuti ndidzamuika kukhala Khalifa pambuyo panga, ndipo ngati Allah Ta’ala atafuna kundifunsa …
Read More »Tafseer Ya Surah Naba
عَمَّ يَتَسَاءَلُونَ ﴿١﴾ عَنِ النَّبَإِ الْعَظِيمِ ﴿٢﴾ الَّذِي هُمْ فِيهِ مُخْتَلِفُونَ ﴿٣﴾ كَلَّا سَيَعْلَمُونَ ﴿٤﴾ ثُمَّ كَلَّا سَيَعْلَمُونَ ﴿٥﴾ أَلَمْ نَجْعَلِ الْأَرْضَ مِهَادًا ﴿٦﴾ وَالْجِبَالَ أَوْتَادًا ﴿٧﴾ وَخَلَقْنَاكُمْ أَزْوَاجًا ﴿٨﴾ وَجَعَلْنَا نَوْمَكُمْ سُبَاتًا ﴿٩﴾ وَجَعَلْنَا اللَّيْلَ لِبَاسًا ﴿١٠﴾ وَجَعَلْنَا النَّهَارَ مَعَاشًا ﴿١١﴾ وَبَنَيْنَا فَوْقَكُمْ سَبْعًا شِدَادًا ﴿١٢﴾ وَجَعَلْنَا سِرَاجًا وَهَّاجًا ﴿١٣﴾ وَأَنزَلْنَا مِنَ الْمُعْصِرَاتِ مَاءً ثَجَّاجًا ﴿١٤﴾ لِّنُخْرِجَ بِهِ حَبًّا وَنَبَاتًا ﴿١٥﴾ وَجَنَّاتٍ أَلْفَافًا ﴿١٦﴾ إِنَّ يَوْمَ الْفَصْلِ كَانَ مِيقَاتًا ﴿١٧﴾ يَوْمَ يُنفَخُ فِي الصُّورِ فَتَأْتُونَ أَفْوَاجًا ﴿١٨﴾ وَفُتِحَتِ السَّمَاءُ فَكَانَتْ أَبْوَابًا ﴿١٩﴾ وَسُيِّرَتِ الْجِبَالُ فَكَانَتْ سَرَابًا ﴿٢٠﴾ إِنَّ جَهَنَّمَ …
Read More »Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2
2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu). Olemekezeka Salmaan Faarsi (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: Ndithu Allah ndi olemekezeka, okoma mtima kwambiri komanso owolowa manja. Ulemu Wake ndiwakuti amaona kuti ndi zotsutsana ndi ukulu Wake ndi chifundo Chake …
Read More »Kuwolowa manja ndi Zuhd (Kudzipatula padziko lapansi) kwa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu)
Nthawi ina, Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) adatenga ndalama za golide mazana anayi, naziika m’thumba napereka kwa wantchito wake: “Pita kwa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) ndipo ukampatse ndalamazi. Ukakafika kumeneko ukadikire kwa kanthawi kuti ukawone zomwe akachite ndi ndalamazo (ndipo ukabwerere ndikundidziwitsa).” Kapoloyo anatenga thumba la ndalama za golide lija napita …
Read More »Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 1
1. Yambani dua pomulemekeza Allah kenako mudzamuwerengera duruud Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam). Pambuyo pake, modzichepetsa ndi ulemu onse, mudzapempha zosowa zanu pamaso pa Allah. Olemekezeka Fadhaalah bin Ubaid (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti nthawi ina Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adakhala munzikiti pamene munthu wina adalowa ndikuyamba kuswali. Kenako adapempha nati: “Oh, …
Read More »