Monthly Archives: July 2024

Anthu Omwe Ma Duwa Awo Amayankhidwa 1

Makolo, Wapaulendo ndi Oponderezedwa Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Ma dua atatu ndi otero kuti pangavute bwanji adzalandiridwa; dua ya bambo (kapena mayi, pa mwana wawo), dua ya musaafir (munthu wapaulendo) komanso dua ya oponderezedwa.”[1] Munthu Osala kudya komanso Mtsogoleri Wachilungamo Olemekezeka Abu …

Read More »

Kulimba Mtima kwa Zubair (Radhiyallahu ‘anhu)

Patsiku la (nkhondo) ya Yarmuuk, ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) adati kwa Zubair (Radhiyallahu ‘anhu): “Bwanji siukupita ndi kukamenyana ndi adani, ndipo ife tidzakutsatira pokalimbana ndi adani.?” Zubair (Radhwiya Allahu ‘anhu) adayankha: “Ndikudziwa kuti ngati ndingapite anthu inu simungagwirizane nane.” Ma Swahaabah (Radhiyallahu ‘anhum) adati: “Ayi, ife tikugwirizana nawe ndipo tikutsatira.” …

Read More »

Kufunika Kwa Dua 3

Njira Yopezera madalitso Ndi kudzitetezera Kwa Adani Olemekezeka Jaabir bin Abdillah akusimba kuti Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adauza maSwahaabah kuti: “Kodi sindingakusonyezeni njira yoti mupulumutsidwe kwa adani anu ndi kulandira zochuluka m’zimene muli nazo? Tembenukirani kwa Allah usiku ndi usana chifukwa dua ndi chida cha okhulupirira.”[1] Mngelo Apangira Dua Munthu …

Read More »

Kuwolowa manja kwa Olemekezeka Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu)

Hishaam bun Urwah akufotokoza kuti ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) okwana asanu ndi awiri adamusankha Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti adzatenge udindo ogawa chuma chawo akadzamwalira. Ena mwa ma Swahaabawa anali Olemekezeka Abdur Rahmaan bin ‘Auf (Radhwiyallahu ‘anhu), Olemekezeka Miqdaad (Radhwiyallahu anhu) ndi Olemekezeka Abdullah bin Mas’uud (Radhwiyallahu ‘anhu) atamwalira, Zubair (Radhwiyallahu …

Read More »

Kukhazikika pa Chisilamu

Abul Aswad akusimba motere. Olemekezeka Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) adamulandira Chisilamu ali ndi zaka zisanu ndi zitatu, ndipo adapanga Hijrah ali ndi zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu. Amalume ake ankamukulunga munkeka ndikumampepelera utsi kuti abanike. Kenako ankamulamula kuti asiye Chisilamu ndipo iye ankayankha kuti: “Sindidzakhala Kaafir! Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) anali …

Read More »

Kufunika Kwa Dua 2

Dua Kupindulira Munthu Mnthawi ino ndi Mtsogolo Olemekezeka Ibnu Umar (Radhwiyallahu anhuma) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Dua imapindulitsa pakalipano komanso mtsogolo. Choncho, inu akapolo a Allah, pirirani popempha.[1] Yemwe amapanga Dua nthawi zonse Amapindula Olemekezeka Abu Sa’iid Khudri (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: …

Read More »

Kukwaniritsa Zomwe Tikuyenera Kumuchitira Allah Ta’ala Komanso Kulemekeza Ma Ufulu A Zolengedwa Zake

M’mbuyomu Chisilamu chisanadze, Uthmaan bin Talhah anali oyang’anira makiyi a Ka’bah Shariif. Amatsegula Ka’bah Lolemba ndi Lachinayi, kuti anthu alowe ndikuchita ibaadah. Nthawi ina, Hijrah isadachitike, pamene anthu ankalowa mu Ka’bah tsiku lawo lomwe adapatsidwa, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) nayenso ankafuna kulowa. Komabe, Uthmaan bun Talhah sanamulore kuti alowe ndipo …

Read More »

Kufunika Kwa Dua 1

Chida cha okhulupirira Olemekezeka Ali (Radhwiyallahu anhu) anasimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati:“Dua ndi chida cha okhulupirira, Mzati wa Dini, ndi Nuur (kuwala) yakumwamba ndi pansi.”[1] Dua ndi gwero la Ibaadah Olemekezeka Anas (radhwiyallahui anhu) akusimba kuti Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adati:”Dua ndiye maziko a ibaadah.”[2] Allah amasangalatsidwa pamene …

Read More »

Kutengapo mbali pa Nkhondo ya Badr

Ismaa’eel bin Abi Khaalid akuti Bahiyy (Rahimahullah) adati: “Panali anthu apakavalo awiri okha omwe ankamenyana ndi adani pa nkhondo ya Badr. Wina adali Olemekezeka Zubair (Radhwiyallahu ‘anhu) yemwe ankalimbana ndi adani kudzanja lamanja, ndipo winayo adali Miqdaad bun Aswad (Radhwiyallahu ‘anhu), yemwe ankamenya nkhondo kumanzere. Hishaam bun Urwah akusimba kuti …

Read More »

Dua

Dua ndi njira yomwe kapolo amadziyandikitsira nayo ku chuma chopanda malire cha Allah. Pali zabwino zambiri zomwe zanenedwa Mmahadith kwa amene amapanga dua. Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adanena kuti dua ndiye maziko a ibaadah zonse. Mu Hadith ina, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adanena kuti Allah amakondwera ndi kapolo amene amapanga …

Read More »