admin

Qiyaam

1. Yang’anani kuchibula. 2. Sungani mapazi pamodzi kapena pafupi momwe mungakwanitsire. Onetsetsani kuti mapazi ayang’ana kuchibla. 3. Pambuyo pake, pangani Niya ya Swalah yomwe mukuswali ndipo kwezani manja anu mpaka zala zanu zazikulu zigwirizane ndi nsonga zamakutu ndipo nsonga za zala zanu zikhale molingana ndi kumtunda kwa makutu anu. 4. …

Read More »

Sayyiduna Umar (Radhiyallahu ‘anhu) Kulamula Zabwino Panthawi Yotsiriza (yamoyo wake)

M’mawa wa tsiku limene Sayyiduna Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) adabayidwa, mnyamata wina adamuyendera nati kwa iye: “Ameer-ul-Mu’mineen! Sangalalani ndi nkhani yabwino yochokera kwa Allah Ta’alal, Inu ndinu Sahaabi wa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) Ndipo inu muli m’gulu la anthu amene adalandira Chisilamu m’masiku oyambirira, ndipo mudasankhidwa kukhala Khalifa ndipo mudachita …

Read More »

Tafseer ya Surah Ikhlaas

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ قُلْ هُوَ اللَّهُ أَحَدٌ ‎﴿١﴾‏ اللَّهُ الصَّمَدُ ‎﴿٢﴾‏ لَمْ يَلِدْ وَلَمْ يُولَدْ ‎﴿٣﴾‏ وَلَمْ يَكُن لَّهُ كُفُوًا أَحَدٌ ‎﴿٤﴾‏ Sura iyi ikufotokoza za chikhulupiriro cha Tawhiyd (umodzi wa Allah Ta’ala mu kakharidwe kake ndi mbiri zake), zomwe ndi gawo limodzi lofunikira kwambiri m’zikhulupiliro zazikulu za Chisilamu. Chikhulupiriro cha Tawheed chinali chinthu chachilendo kwa …

Read More »

Swalaah Isanayambe

1. Chisamaliro chapadera chiyenera kutengedwa povala moyenera pa Swalaah. Mkazi ayenera kuvala chovala choterocho chomwe chidzabisa thupi lake lonse ndi tsitsi lake. Ndikusadzipatsa ulemu iye mwini kuvala zovala zothina zomwe zimasonyeza mmene thupi lake lilili kapena kuvala zovala zopyapyala zimene zingachititse kuti ziwalo zenizeni ziwonekere. Ngati chovalacho chili chooneka kuti …

Read More »

Hazrat Umar (radhwiyallahu anhu) Kufuna kuyikidwa pafupi ndi Rasulullah (swallallaahu alaih wasallam)

      Pakati pa mphindi zomaliza pambuyo pa Hazrat Umar (radhiliyalahlah ‘Ahu) adaphedwa mwangozi, Anatumiza mwana wake, Hazrat Abdullah Bin Umar (radhwiyallahu ‘Anhuma), kunyumba kwa Hazrat Aaishah (radhiyallahu ‘ahha). Hazrat Umar (Radhiyallahu anhu adamulangiza iye kuti ukamuuze kuti Umar akupereka Salaam. Usakanene kuti Amiirul muuminiin popeza kuyambira lero sindidzaitanidwanso …

Read More »

Kudzichepetsa kwa Sayyiduna Umar (Radhwiyallahu ‘anhu)

Olemekezeka Miswar bin Makhramah (radhwiyallahu ‘anhu) akusimba kuti pamene Umar (radhwiyallahu ‘anhu) anabayidwa, iye anayamba kumva chisoni ndi kukhala ndi nkhawa kwambiri kuudandaulira ummah. Ibnu Abbaas (radhwiyallahu ‘anhu) adamtonthoza nati: “Oh Ameer-ul-Mu’mineen! Palibe chifukwa chodandaulira. Mudakhala pamodzi ndi Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndipo mudakwaniritsa ma ufulu ake onse . Ubwenzi …

Read More »

Mfundo Ya Imaam Shaafi’ee

Imaam Shaafi’e (rahimahullah) walemba mu chitabu chotchedwa Ikhtilaaful Hadith kuti: Sitikudziwa mwa akazi olemekezeka a Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) kusiya nyumba zawo ndikupita kunzikiti kukaswali Swalaah ya Jumuah kapena Swalah ina iliyonse, ngakhale kuti adali akazi olemekezeka a Sayyiduna Rasulullah chifukwa cha udindo wawo wapadera ndi ubale wawo ndi Mtumiki …

Read More »

Ulemu wa Umar (radhwiyallahu ‘anhu) kwa Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu)

Hazrat Umar (radhiyallahu anhu) nthawi zonse ankavomereza udindo wapamwamba wa Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo sankadzitenga ngati iye ndi wofanana ndi  Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu). Ulendo wina gulu la anthu linamutamanda  Umar (radhwiyallahu ‘anhu) ponena kuti: “Ndikulumbirira kwa Allah! Sitinaonepo munthu wolungama, wonena zoona, ndi wokhwimitsa zinthu kwambiri kwa …

Read More »

Zul Hijjah – Mwezi wa Haji ndi Qurbaani

Zul Hijjah ndi mwezi womaliza wa kalendala ya Chisilamu. Ngakhale mwezi wonse wa Zul Hijjah ndi wopatulika komanso wodalitsika, masiku khumi oyambirira a Zul Hijjah ali ndi kupatulika kwakukulu ndi ubwino. Ponena za masiku khumi oyambirira a Zul Hijjah, Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam wasallam) adati: “Masiku abwino kwambiri padziko lapansi …

Read More »

Kukhudzika kwa Sayyiduna Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) pa Swalaah

M’mawa womwe Umar (radhwiya allaahu ‘anhu) adabayidwa, Olemekedzeka Miswar bin Makhramah (radhwiyallahu ‘anhu) adadza kudzamuona. Polowa mnyumba adapeza Umar (radhwiyallahu ‘anhu) atafunditsidwa ndi ndi nsalu ali chikomokere. Olemekezeka Miswar (radhwiyallahu ‘anhu) adafunsa anthu omwe adalipo pamenepo kuti, “Ali bwanji?” Iwo anayankha kuti: “Ali chikomokere monga mukuwoneramu.” Chifukwa panalibe nthawi yochuluka …

Read More »