Salaam ndi moni wa Chisilamu. Monga momwe Chisilamu chimatanthauza mtendere, moni wa Chisilamu ndi moni wamtendere komanso ofalitsa uthenga wamtendere. Salaam ndi imodzi mwa zochitika zachisilamu zomwe ndi chizindikiro cha Msilamu, ndipo kufunika kwake kwatsindikitsidwa kwambiri mahadith. Olemekezeka Abdullah bin Salaam (Radhwiyallahuanhu) akuti: Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale pa iye) …
Read More »Nkhumbo lalikulu la Olemekezeka Saiid bin Zaid (Radhwiya Allaahu ‘anhu) lopereka Moyo Wake Munjira Ya Allah.
Mzinda wa Damasiko utagonjetsedwa ndi Asilamu, Abu Ubaidah (radhwiyallahu ‘anhu) mkulu wa asilikali achisilamu -anasankha Sa’iid bin Zaid (radhwiyallahu ‘anhu) kukhala kazembe wa mzinda wa Damasiko. Pambuyo pake Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) adapitilira ndi gulu lake lankhondo kulowera ku Jordan. Atafika ku Yordan, anamanga msasa kumeneko ndi kuyamba kukonzekera zolimbana …
Read More »Kutonthoza Oferedwa
13. Sizoloredwa kupita ku nyumba ya kafiri yemwe wamwalira kukapepesa mwambo wamaliro uli mkati. Koma akakhala kuti ndi kafiri oyandikana naye nyumba kapena kaafir aliyense amene wataya wachibale wake, mwachitsanzo, mwana, ukhoza kumutonthoza ndi mawu awa: أَخْلَفَ اللّه عَلَيْكَ خَيْرًا مِنْهُوَاَصْلَحَكَ Akhlafa Allahu ‘Alayka Khayran Minhu Wa ‘Aslahaka Allah akupatse …
Read More »Zida Zikuluzikulu za Dajjaal – Chuma, Akazi ndi Zansangulutso
Dajjaal akadzaonekera padziko, zida zikuluzikulu zomwe adzagwiritse ntchito kusocheretsera munthu ndi chuma, akazi ndi zansangulutso. Allah Ta’ala adzamupatsa mphamvu yochita zozizwitsa kotero kuti onse amene azidzaziona adzakopeka ndi kutengeka ndi fitnah (Mayesero) ake. Allah Ta’ala adzamloleza kugwetsa mvula, kupangitsa nthaka kutulutsa mbewu, ndipo chuma cha m’nthaka chidzamtsatira kulikonse kumene azidzapita. …
Read More »Hazrat Sa’eed bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) Kuteteza maSwahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum)
Nthawi ina Mughiirah bin Shu’bah (Radhwiyallahu ‘anhu) atakhala pamodzi ndi anthu ena mu Musjid ya ku Kufah, Sa’eed bun Zayd (radhwiyallahu ‘anhu) adalowa mu mzikiti. Mughiirah (Radhiyallahu ‘anhu) adamulonjera ndipo mwaulemu adamupempha kuti akhale pansi pa nsanja yomwe idali patsogolo pake. Patapita nthawi pang’ono, munthu wina wa ku Kufah adalowa …
Read More »Hazrat Sa’iid bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) Apirira ku Mavuto Chifukwa Chachisilamu.
Hazrat Umar (radhwiyallahu ‘anhu) – munthu yemwe dzina lake loyera ndi njira yolemekezera chisilamu, ndipo changu cha imaani chinali chotere mpaka lero, patadutsa zaka 1300, anthu osakhulupirira amamuopabe,adali otchuka chifukwa chowazunza Asilamu (iyeyo) asanalowe Chisilamu. Adapitilizanso kufunafuna mipata yomupha Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam). Tsiku lina maquraish adasonkhana. …
Read More »Kumuzindikiritsa Mwana Kwa Allah
Kulera mwana n’kofunika kwambiri ndipo tingakuyerekezere ndi maziko a nyumba. Ngati maziko a nyumba ali olimba, ndiye kuti nyumbayo idzakhalanso yolimba ndipo idzapirira ku nyengo iliyonse. Mosiyana ndi zimenezi, ngati maziko a nyumbayo ndi ofooka komanso ogwedezekagwedezeka, ndiye kuti ndi kugwedezeka pang’ono, nyumbayo idzagwa. Chimodzimodzinso, kulera mwana ndiko maziko amene …
Read More »Kutonthoza Oferedwa
7. Nkoloredwa kuyamikira omwalirayo. Komabe, pomutamanda, onetsetsani kuti simukukokomeza kapena kumutamanda pa makharidwe amene panalibe mwa iye. Momwemonso musatengere chikharidwe ndi njira za makafiri pomutamanda. 8. kuchuluka kwa nthawi ya ta’ziyat ndi masiku atatu kuchokera tsiku lomwalira. Pambuyo pa tsiku lachitatu, ndi makruh kupanga ta’ziyat. Komabe, ngati munthu sadathe kubwera …
Read More »Ma Sunnah Komanso Miyambo Yochezera Ndi Namfedwa
1. Ta’ziat imatanthauza kugawana chisoni ndi ananfedwa ndi kuwamvera chisoni pa kutaika kwa okondedwa wawo. Izi zimachitika pomupangira dua omwalirayo pamaso pa akubanja ake. Momwemonso izi zidzachitika polipangira Dua banja lake, kupempha Allah Odalitsika ndi Wapamwambamwamba, kuti awadalitse powapatsa kupilira ku mayesero amenewa. 2. Dua ingachitike m’mawu awa: “Allah amupatse …
Read More »Dua ya Hazrat Said bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) Iyankhidwa
Nthawi ina, Arwa bint Uwais, neba wa Hazrat Said bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu), adadza kwa Muhammad bin ‘Amr bin Hazm (Rahimahullah) ndi dandaulo lokhudza neba wake Hazrat Sa’eed bun Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu). Ananena kuti adamanga khoma lake m’malo mwake ndipo adapempha Muhammad bin Amr (Rahimahullah) kuti apite kwa iye kuti …
Read More »
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu